Nkhani

Mwambo wogwetsa simba

Listen to this article

Sukulu zatsekera ndipo zikatere m’maboma ambiri makolo ali kalikiriki kukonzekera kuti ana awo apite kusimba kukavinidwa. Kumenekotu kumakhala uphungu kuti anawa adziwe khalidwe komanso momwe zina za m’banja zimakhalira. Zambiri zakhala zikukambidwa zokhudza unamwaliwu koma sabata ino BOBBY KABANGO akutibweretsera mwambo womwe umachitika pamene anamwali akutulutsidwa kusimba pachinamwali cha jando. Kodi zimakhala bwanji?simba

Tidziwane…

Ndine Evason Chalamanda, wamkulu wa simba muno m’mudzi mwa Malika, kwa T/A Mpama m’boma la Chiradzulu. Ngati mukufuna kudziwa chilichonse cha simba, ine ndiye mwini wake.

 

Timamva kuti kumakhala mwambo patsiku lomwe mukusasula simba, kodi ndi zoona?

Zimenezo ndi zoonadi, chinamwali ndi mwambo ndiye pamene mwamaliza kulanga anamwali, mumayeneranso kuti mutsate mwambo womwewo ngati mukusasula simba. Ndigwirizane nanu kutidi pamakhala mwambo.

 

Umakhala mwambo wanji?

Mwambo wosangalala basi, kuti tamaliza chinamwali. Tikawasunga anamwaliwa kwa sabata zitatu, ndiye tsiku lomwe tikuwatulutsa timayenera kukhala ndi mwambo basi.

 

Mwambowo umachitikira kuti?

Malo alionse oyandikana ndi simbalo koma usachitikire kunyumba. Mumangotuluka kusimbako ndi kukhala chapafupi ndi simbalo. Mwambowu suchitikira kusimba chifukwa kumakhalabe anamwali. Dziwani kuti mwambowu ukamayambika anamwali amakhala asanatulutsidwe ndipo amadzakupezani mwambowo uli mkati. Komanso dziwani kuti amayi ndi anthu amene sadavinidwe sayenera kufika kusimbako n’chifukwa mwambowo suchitikira kumeneko.

 

Bwanji osangopangira kusimba komweko?

Pamene tikusasula simba, timafuna tisangalale ndi anzathu. Makolo, achibale komanso anzathu kuchokera midzi yosiyanasiyana amabwera. Poti anthuwa saloledwa kufika kusimba, n’chifukwa chake timachoka kusimbako kuti tikumane malo abwino. Anthuwa amakhala akufupa anamwaliwa pamene atuluka kusimbako.

 

Kodi kumakhala zochitika zotani patsikuli?

Aliyense amachita monga akufunira koma kunoko timakhala ndi mwambo wosangalala ndi magule, timakhala ndi azungu komanso chinyama zomwe zimasangalatsa anthu amene abwera kudzaonerera mwambowo.

 

Azungu?

Eya, kapena kunena kuti anthu amene khungu lawo ndi loyera.

 

Amachokera kuti?

Amachokera kusimba komweko!

 

Ndi a m’dziko lomwe lino? Kapena mumachita kupangatu inu…

Ndi anthu amene amakhala kusimbako koma amakhala kuti adavinidwa kale. Awa si anamwali chifukwa anamwali amatuluka usiku basi, pamenenso kumakhala mwambo wina.

 

Kodi ndi azungudi? Kapena mundipusitsatu…

Amenewa si azungu enieni, timachita kupanga kusimba komweko. Timatenga dothi n’kuliviika m’madzi. Likafewa timawauza kuti ayambe kudzola thupi lonse ndipo likauma munthuyo amafanana ndi mzungudi.

 

Amaoneka bwanji?

Khungu ngati mzungu, koma mavalidwe ndiye amavala zosiyasiyana chifukwa ena amavala nsalu, ena dilesi ndiye amaoneka ngati atsikana koma onse ndi anyamata.

 

Ndiye mwati kumabweranso chinyama?

Eya ndipo chimakhala chofanana ndi mbalame. Dzina lake timachitcha chimwanambera. Ntchito yake n’kuopseza ana kuti adziwe za kuopsa kwa samba. Paja ndanena kuti kumabweranso ana koma sikuti chimawamenya.

 

Mumachitanso kupanga?

Eya, timachipanga ndi mitengo, kunjako timachikutira ndi bulangete kapena nsalu. Mkatimo mumakhala anthu awiri kapena mmodzi kuti azichiyendetsa.

 

Cholinga chimakhala chiyani?

Cholinga n’kufuna kuti anthu amene abwerewo kudzaonera akhale ndi chidwi ndipo asangalatsidwe. Zikamatere timapeza ndalama zambiri chifukwa kumabwera anthu ambiri ofuna kudzaonera mwambowo. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »