Chichewa

Mwana wa zaka 13, mavuto osakata

Ikakuona litsiro mvula siyikata. Mwambiwu wapherezera pa msungwana wina wa Sitandade 7 (yemwe sitimutchula dzina) pasukulu ina ku Chikwawa.

Izi zidadziwika achipatala atamupeza msungwanayo ndi chinzonono komanso mabomu potsatira kumuyeza mkulu wina atamugwirira kochapa. Mwanayo adapezekanso ndi kachirombo ka HIV. Pano anzake, ngakhalenso abale ake, akumusala, mpaka kukana kudya naye mbale imodzi; ngakhalenso kusewera naye chifukwa cha momwe m’thupi mwake mulili.

Mwanayo lero chidwi cha sukulu chikuzilala

Pamapeto pake, aphunzitsi akuti chidwi cha mwanayo, yemwe ali ndi zaka 13, pamaphunziro chikulowa pansi, kupereka chiopsezo choti angalephere kukwaniritsa loto lake lodzakhala woimira ena pamilandu—loya.

Mavuto a mwanayo adafika pena pa 21 January chaka chino, pomwe adapita kukachapa mmalo mopita madzi othirira madimba a nzimbe za kampani ya Illovo m’bomalo.

Apo n’kuti m’mudzi mwa mwanayo mulibe mjigo.

Kenaka, mwanayo akuti adangomva kuti tswereee! Bambo wina kutulukira mumzimbe tsidya linalo, n’kudumphira m’madzimo ngati akungofuna kusambira. Koma adasambira mpaka kuoloka kufika tsidya lomwe kudali mwanayo.

“Adandiopseza ndi mpeni. Adati ndisakuwe chifukwa adati andipha. Kenaka, adavula malaya. Adanena kuti nanenso ndivule ndipo ndigone pansi,” mwanayo adafotokoza, atazyolika.

Iye adaonjeza kuti bambo amene ndi wochokera m’mudzi mwawo ndiye adamuchita chipongwecho.

“Ndinkamva kupweteka, koma ndinkangolira pansipansi chifukwa ndimaopa,” mwanayo adafotokoza Lolemba lapitali pomwe mtolankhani wathu adalowera ku Chikwawa kuti akamve zovuta zimene zadza kaamba ka kusefukira kwa madzi.

Mwanayo, yemwe ndi nzime m’banja la ana atatu, adati bamboyo adatenga nthawi kuchita zachipongwezo, ndipo atamaliza adamuuza mwanayo kuti asakauze aliyense.

Kuchapa kudathera panjira. Iye adati atafika kunyumbako sadauze mayi ake zankhaniyo. Atapita kusukulu adakauza aphunzitsi ake amene adatengera nkhaniyo kwa makolo komanso kupolisi.

Apo mpamene bamboyo, Kennedy Chiseko wa zaka 36 yemwe amakhalanso m’mudzi mwa mwanayo, adanjatidwa.

Ndipo nkhaniyi ndiyo  mwanayo adakanena popereka umboni wake pamaso pa Gladstone Chirundu yemwe pa 11 March adagamula kuti Chiseko akasewenze zaka 8 kundende, atamupeza wolakwa pamlandu wogwirira mwana mosemphana ndi Gawo 138 la malamulo a dziko lino.

Komatu mwanayo akadamuyeza kaye ngati adapatsidwa kachirombo koyambitsa matenda a Edzi kuti achipatala amupatse mankhwala ochotsa HIV pasanathe maola 72 kuchokera pamene anagwiriridwa. N’chifukwa chiyani izi sizinachitike?

Malinga ndi mneneri wapolisi ku Chikwawa, Foster Benjamin, padalibe danga loti n’kutero, chifukwa nkhani ya mwanayo idafika kupolisi patadutsa maola 72.

“Pokauza aphunzitsi ake kuti wachitidwa chipongwe nthawiyo idali itadutsa,” adatero iye.

Malinga ndi aphunzitsi komanso bambo amwanayo, atamva za kugwiriridwa kwake adathamanga naye kuchipatala komwe zidasonyeza kuti adagwiriridwadi ndipo adawauza kuti apitenso. Atapitanso patatha milungu iwiri, achipatala adapeza kuti adali ndi matenda opatsirana pogonana a chinzonono ndi mabomu komanso kachirombio koyambitsa matenda a Edzi.

Malinga ndi lamulo limene Nyumba ya Malamulo  idakhazikitsa chaka chatha, lokhudza matenda a Edzi, n’kovuta kupereka umboni woti ‘wakuti ndiye adapatsira wina kachirombo ka HIV’ choncho Aphungu adachotsa mfundo yonena kuti amene akukaikiridwa kuti adapatsa wina kachiromboka azizengedwa mlandu.

Kuchoka pa nthawi yomwe mwanayo adauzidwa ndi a chipatala kuti ali ndi kachiromboka mpaka lero, moyo wake wakhala wodzadza ndi mavuto.

Iye adati kunyumba kwawo abale ake amakana kudya naye mbale imodzi ponena kuti awapatsira matenda.

“Anzanga amene ndimacheza nawo pano sacheza nanenso. Ndimakhala ndekha, amandiimba nyimbo kuti ‘wa Edzi uyo’,” adatero iye.

Aphunzitsi akewo adati zomwe akulimbana nazo pano ndi kusalidwa komwe mwanayo akukumana nako.

“Tsiku lina adafika kunyumba kwanga akulira. Amati abale ake akumunena komanso kunyumba kwawo akumukaniza kudya nawo moti amati adagona osadya,” adatero mphunzitsiyo amene adati chidwi ndi khama la mwanayo pasukulu zayamba kuchoka.

Bambo a mwanayo

Related Articles

Back to top button