Chichewa

‘Mwayi kuthima kwa magetsi’

Listen to this article

 

Pomwe ena akudandaula za kuthimathima kwa magetsi, ena akusimba lokoma kuti adapatirapo mwayi wabanja.

Victor Mpunga yemwe pa 28 December 2015 adapanga chinkhoswe ndi Mary Makhiringa, akuti adayamba kulankhulana pagolosale pomwe Mary amakagula chakudya atachita ulesi kusonkha moto magetsi atathima.

Victor ndi Mary adakumana pagolosale
Victor ndi Mary adakumana pagolosale

Victor akuti nthawi zambiri amakonda kucheza pagolosale yamnzake pafupi ndi pomwe Mary amakhala ndipo amangomezera malovu msungwanayu akamadutsa popita ndikuchokera kuntchito.

Iye akuti mwayi udapezeka tsiku lina madzulo magetsi atathima pamenepo Mary akuchokera kuntchito ndipo mmalo mosonkha moto kuti aphike nkhomaliro, adangoganiza zokagula chakudya pagolosaleyo ndipo nkuti Victor ali pomwepo.

“Ndidangoti bowa bwanga nthawi yomweyo nkuyambitsa macheza. Ndimaona ngati andinyoza malinga ndi mmene amaonekera koma ayi ndithu tidacheza bwinobwino mpaka chinzake chidayamba,” adatero Victor.

Iye adati chinzakecho padali polowera chabe chifukwa patangotha nthawi pang’ono chibwenzi chidayamba mpaka makolo kudziwitsidwa nkuyamba kupanga dongosolo la chinkhoswe.

Iye adati ulemu amamusangalatsa kwambiri chifukwa cha mawonekedwe, khalidwe ndi luntha pofuna kupanga chinthu ndipo salola kupanga chinthu chomwe sakuchimvetsetsa zomwe iye amaona ngati mphamvu.

Mary adati kwa iye chachikulu nchakuti Mulungu adamulozera mwamuna yemwe amayembekezera moti ali ndi chiyembekezo chakuti adzakhala pabanja lokoma ndi losangalatsa kwambiri.

“Ndimamukonda kwambiri Victor chifukwa ndi mwamuna wachitukuko. Ndi munthu uja oti akaganiza kapena kunena chinthu amayesetsa mpaka chichitike basi ndiye ndimadziwa kuti ali nkuthekera kwakukulu,” adatero Mary.

Awiriwa akuti akuyembekezera kumanga ukwati woyera chaka chino cha 2016 ndipo zokonzekera zili mkati.

Victor amachokera m’mudzi mwa Muona T/A Mulolo m’boma la Thyolo pomwe Mary amachokera m’mudzi mwa Mpombwe T/A Mkanda m’boma la Mulanje koma onse akukhala mumzinda wa Lilongwe. n

Related Articles

Back to top button