ChichewaNational News

Ndale zogawanitsa miyambo zanyanya

Listen to this article

Si zachilendonso kumva kuti andale adzetsa ziwawa pamwambo wachikhalidwe. Lamulungu, kudali gwiragwira kokhazikitsa mwambo wag ulu la Ayao lomwe likutchedwa Chiwanja Cha Ayao.

Pamwambowo, wothandizira wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima adamunjata pomuganizira kuti amachita zokaikitsa.

Othandizira Chilima (pakati) adamangidwa ‘pochita zokaikitsa’

Anthuwo ati adali ndi mphatso yochoka kwa Chilima koma adalephera kupereka chifukwa cha zovuta zina.

Izi zimachitika patangotha mwezi, patabukanso chisokonezo pamaliro a Themba la Mathemba Chikulamayembe m’boma la Rumphi.

Mpungwepungwe udadza pamene ampingo adalandidwa chimkuzamawu pamene amapereka mpata kwa Chilima ndi mtsogoleri wa zipani zotsutsa Lazarus Chakwera kuti alankhule.

Nakonso ku mwambo wa Gonapamuhanya wa Atumbuka kwakhala kukuchitika zisokonezo zodza ndi andale kwa zaka ziwiri zotsatizana.

Mmalo mopitira zomwe ayitanidwira, andalewo amafuna kupikisana ku miyamboyo ndipo salola kugonjerana.

Polankhulapo pa mchitidwewo, kadaulo wa ndale pa sukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia George Phiri adati vuto lalikulu limabwera chifukwa okonza miyamboyo amapereka gawo lalikulu kwa andale.

Phiri adapereka chitsanzo cha mwambo wa kulamba omwe Achewa amakonza m’dziko la Zambia komwe ngakhale kumapita andale, sapatsidwa mphanvu.

Iye adati izi zimathandiza kuti kumaloko kusakhale mpikisano ndi kudzionetsera pakati pa zipani.

“Achikhalidwe azionetsetsa kuti mwambowo uli m’manja mwawo osati kuwapatsa andale,” adalongosola Phiri.

Iye adatinso vuto lina limadza maka andalewo akatenga gawo lalikulu popereka thandizo lokonzera mwambo wa mtunduwo.

“Tiyeni tisiye zomachita ndale paliponse chifukwa zikuononga chikhalidwe. Tizilekanitsa zinthuzi,” adatero Phiri.

Naye mbusa Macdonald Sembereka yemwe ndi mmodzi wa akuluakulu omwe adakonza mwambo wa Chiwanja cha Ayao adati vuto la andale ndi loti amafuna kudzionetsa kuti wa mkulu mndani ku miyambo yachikhalidwe.

Sembereka adati andalewo amaphangira ku zochitikazo mpaka kuononga miyambo ya chikhalidwe.

“Khalidwe ili silikuthandiza chikhalidwe chathu. Tikuwapempha kuti asamapezerepo mpata wotsatsa malonda awo pa miyamboyo,” adatero Sembereka.

Iye adatinso andalewo ngofunika kulolerana pa nthawi ngati imeneyo ndipo adapereka chitsanzo cha mtsogoleri wopuma wa dziko lino Joyce Banda yemwe ngakhale ali wa mtundu wa Chiyao sadakhale nawo.

“Anthufe tikungoyenera kudziwa kuti chikhalidwe nchachikulu kuposa ndale ndipo ndale zikufunika kulamulilidwa ndi chikhalidwe,” adatero Sembereka.

Wapampando wa gulu losunga chikhalidwe cha Achewa, Kanyama Phiri adati gululo limakana kutengapo gawo pa ndale chifukwa malamulo awo ochokera kwa Gawa Undi sawavomereza kutero.

Phiri adati popewa andale kuwasokonezera zachikhalidwe chawo, gululo amakakumana kwa Gawa Undi basi.

“Palibe cholakwika kuwaitana andalewo koma mpofunika kukhazikitsa ndondomeko zoti azitsatira akafika pamalowo,” adatero Phiri.

Naye Gogo Chikalamba Gondwe yemwe amakonza mwambo wa Atumbuka wa Gonapamuhanya omwe wakhala ukukumana ndi mazangazime chifukwa cha andale, adati gulu lawo tsopano lidaika ndondomeko zomwe andalewo amatsatira popewa chisokonezo.

“Komabe tinene kuti nthawi zambiri tikayandikira nthawi yosankha atsogoleri, andalewo amalowerera ndithu cholinga choti anthu awadziwe,” adatero Gondwe.

Iye adati gulu lake lidawauza andalewo kuti akamapita ku mwambo wa Gonapamuhanya, azikangoonera osati kuchitapo ndale.

Mitundu yambiri m’dziko muno ili ndi magulu ake osungitsa chikhalidwe omwe ena mwa iwo akhala akusokonekera chifukwa cha mikangano ya andale. n

Related Articles

Back to top button