Chichewa

Ngozi zanyanya chaka chino—Apolisi

Listen to this article

 

Apolisi ati ngozi za pamsewu m’dziko muno zachuluka ndi 18 pa ngozi 100 zilizonse poyerekeza ndi chaka chatha nyengo ngati yomweyi.

Mkulu wa apolisi m’chigawo cha pakati, George Kainja, ndiye adanena izi Lachinayi potsegulira msonkhano wa komiti yoyang’anira za chitetezo cha m’mudzi kulikulu la polisi m’chigawo chapakati.

Iye adati chomvetsa chisoni n’chakuti ngozi zambiri zimakhudza ana asukulu ndi akabaza ndipo zimachitika kwambiri chifukwa chosatsatira malamulo a pamsewu ndi kuyendetsa galimoto zosayenera kuyenda pamsewu.

Kainja: Apolisi ena akuipitsa mbiri ya polisi
Kainja: Apolisi ena akuipitsa mbiri ya polisi

“Taluza miyoyo yambiri chifukwa cha ngozi za pamsewu koma kufufuza, zambiri mwa ngozizi zimachitika chifukwa chophwanya malamulo a pamsewu ndi kugwiritsa ntchito galimoto zosayenera kuyenda pamsewu,” adatero Kainja.

Iye adati nthawi zina galimoto zosayenera kuyenda pamsewu zimapezeka pamsewu kaamba ka ziphuphu zomwe apolisi apamsewu amalandira kwa oyendetsa ndi eni ake magalimoto kuti asawagwire.

Kainja adadzudzula mchitidwe wa ziphuphu za pamsewu kuti zimabwezeretsa chitukuko cha dziko mmbuyo komanso zimaononga mbiri ya polisi.

“Anthu podzudzula amangoti apolisi, osasiyanitsa kuti apolisi ake ati. Posachedwapa kwatuluka malipoti angapo omwe akusonyeza kuti m’polisi mukuchitika zachinyengo kwambiri ndipo ili si bodza,” adatero Kainja.

Mkuluyu adapempha komiti yoyang’anira ntchito zachitetezo cha m’mudzi kuti azilimbikitsa ntchitozi kuti chitetezo chizipita patsogolo chifukwa apolisi alipo ochepa kuyerekeza ndi momwe zimafunikira.

Iye adati chigawo cha pakati chokha chili ndi apolisi 451 omwe amayembekezeka kuteteza anthu oposa 7 miliyoni kutanthauza kuti wapolisi mmodzi amateteza anthu 1 600 mmalo mwa anthu 500 pamalamulo a mgwirizano wa maiko.

Iye adatinso mchitidwe wozunza maalubino udakula m’chakachi kaamba ka mphekesera zakuti mafupa a anthuwa ndi amtengo wapatali ndipo adati iyi ndi ntchito ya anthu kudzera m’magulu a chitetezo cha m’mudzi kuteteza anthuwa.

Related Articles

Back to top button