Nkhani

Njala yavuta, mafumu achenjeza

Listen to this article

Mafumu ena m’dziko muno apempha boma kuti liwathandize kuthana ndi njala yomwe yayamba kale kusautsa maboma angapo ndipo madera ena ayamba kale kupulumukira zikhawo.

Mafumuwa ndi T/A Kachindamoto ku Dedza, Tengani ku Nsanje ndi Mlauli ku Neno.

Izi zikudza patangodutsa sabata ziwiri a bungwe lounikira ndi kuchenjeza za njala la Famine and Early Warning Systems Network (Fewsnet) litachenjeza kuti pafupifupi anthu 1.7 miliyoni asowa chakudya m’dziko muno chaka chino.

Lipoti la bungweli linaunikira za kapezekedwe ka chakudya m’dziko muno kuyambira mwezi wa Ogasiti chaka chino mpaka Malichi chaka cha mawa. Kuunikiraku kunatinso ntchito zolimbana ndi njalayi zikuoneka kuti n’zosakwanira kwenikweni ndipo zingakhale zitagugiratu pofika Novembala kapena Disembala chaka chino.

Poonjezera, zounikirazi zinati mwa maboma okhudzidwa ndi Nsanje, Chikhwawa, Balaka, Blantyre, Phalombe, Machinga, Zomba, Thyolo, Mulanje, Neno, Mwanza, komanso Mangochi ku chigwawo cha kummwera, Salima ndi Ntcheu pakati komanso mbali zina m’dera la kumpoto m’boma la Karonga kumpoto.

T/A Kachindamoto wati kumeneko midzi 300 yomwe muli anthu pafupifupi 70 000 yakhudzidwa ndi njalayo.

“Tidali ndi msonkhano ndi a bungwe la zaulimi ndipo tidapeza kuti tikufunika [thandizo la] matani 1 000 a chimanga. Tidayesera ulimi wa mthirira koma zakanika chifukwa mitsinje yaphwa.

“Ngati sitingalandire thandizo mpaka Disembala, chiyembekezo chilipo kuti anthu ataya miyoyo,” yatero mfumuyo.

Kachindamoto wati njalayi yagwa kaamba kosowekera mvula m’madera angapo komanso kuchuluka kwa mvula m’madera ena.

“Tidabzala kawiri kaamba ka vuto la mvula koma sizidaphule kanthu.Kumapeto n’komwe kudabwera mvula yambiri mpaka madzi kusefukira,” adatero Kachindamoto.

T/A Tengani wati galu wakuda sadasiye malo pomwe anthu 20 000 pansi pake akhudzidwa ndi njalayi. Vuto kumeneko akuti lidali lakusowa kwa mvula.

“Tidafika potopa kulankhula za njala kuno.Boma litithandize ndi zipangizo kuti tiyambe ulimi wa mthirira chifukwa pafupifupi dera lililonse kuno lakhudzidwa ndi njala,” idatero mfumuyi yomwe yati dera lake lili ndi anthu pafupifupi 35 000.

Iye wati posakhalitsapa ena ayamba kudya nyika chifukwa chosowa pogwira. Tengani adati madera ena kumeneko ayamba kale kulandira ufa ndi thandizo lachimanga.

T/A Mlauli wati ku Neno mvula siidagwe bwino ndipo njala yakhudza pafupifupi boma lonse.Mlauli wati m’mudzi mwake muli anthu 25 903 ndipo pafupifupi onse akhudzidwa ndi njalayo.

“Tikufuna thandizo mwachangu,” adatero Mlauli.

Mkulu wa bungwe loona za ndondomeko za ulimi lomwe si laboma  la Civil Society Agriculture Network (Cisanet), Tamani Nkhono-Mvula, wati alandilapo malipoti kuti mabomawa akhudzidwa ndi njala.

Iye wati kotero boma likuyenera kuvomereza kuti m’dziko muno muli njala n’cholinga choti mabungwe ayambe kuthandiza. Iye adati mabungwe ali chile kuthandiza anthu koma pena amadikira boma livomereze za vuto lomwe lagwalo.

“Pena atsogoleri amatha kuvomereza kapena kukana kuti kulibe njala pazifukwa za ndale ndipo mabungwe amakhala omangika kuyamba kuthandizapo.

“Chakudya m’dziko muno chilipo. Chiyembekezo chilipo kuti anthuwa apulumutsidwa,” adatero mkuluyu.

Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, wati boma layamba kale kugawa chakudya m’madera ena omwe akhudzidwa ndi njalayi kotero madera omwe sadalandire thandizoli akuyenera kudziwitsa boma.

Iye wati m’sabatayi madera ena okhudzidwa ndi njalayi m’boma la Blantyre ndi amene amalandira thandizoli.

Malinga ndi unduna wa zamalimidwe, dziko lino lidakolola matani 3.6 miliyoni a chimanga pomwe dziko lino limafunika matani 2.8.

Chiyambire malipoti a njalawa, bola lakhala likutsutsa, ati dziko lino lili ndi chakudya chokwanira.

M’mbuyomu, Nduna ya Mapulani a Chuma ndi Chitukuko, Atupele Muluzi, inati kuunikira kwa Fewsnet kunali kosadalirika, ati m’dziko muno muli ndondomeko yomwe ingadziwe bwino za chiwerengero chomwe chili pa chiopsezo cha njala.

Mu Julaye chaka chino, ndondomekoyo inati anthu 1.63 miliyoni ndi omwe anali pa chiopsezo.

Chiopsezochi chikudza pomwe dziko lino likukumbukira tsiku lachakudya padziko lapansi, tsiku lomwe limakumbukukiridwa ndi mayiko oposa 150.

Tsikuli lomwe limakumbukiridwa pa 16 Okutobala likukumbukiridwa pamutu woti ‘Mgwirizano wa mabungwe azaulimi; ngodya yodyetsera dziko.’

 

Related Articles

Back to top button
Translate »