Chichewa

Njoka zoweta ndi penshoni

Pa Wenela tsikulo padafika ng’anga ina imene inkati yangofika kumene kuchokera ku Mozambique, inde dziko la nkhondo.

TADEYO

Ng’angayo idafika ndi chikwama chake chasaka momwe idatulutsa njoka zingapo—mphiri, nsato, mbobo, nalikukuti, mamba ngakhalenso chilere, njoka yopanda ululu.

Ankafanana ndithu ndi Moya Pete. Kulankhula, chimodzimodzi.

“Ku Tete ndabwerako. Ndathawa nkhondo kwambiri. Ndabwera ndi njoka zoweta,” adatero mkuluyo.

“Akulu, njoka yoweta sagula pamsika, nanjinanji wa ku Mozambique!” adatero Abiti Patuma.

“Ukunama kwambiri. Izi ndi njoka zowetedwa nthawi ya Machel, Chissano, Guebuzza ndi uyu winayu. Kaya mukuti ndani uyu. Mwana wa ndani uyu,” adatero sing’anga uja.

Abale anzanga, tidaona zozizwitsa. Njoka imodzi idayangata mwendo wake n’kulowa mkabudula mwake n’kutulukira kwinako, n’kukazinga mutu wake. Ina idachoka paphewa, kulowa m’kabudula, n’kukazinga mwendo. Njoka saweta.

“Akulu, kodi njokazi mukufuna mutikawe, kapena chiyani?” adafunsa Abiti Patuma.

“Adakuuzani kuti njoka saweta adakunamizani kwambiri. Izi ife a namanyonyoro timaweta kwambiri kwathu ku Cholo,” adatero sing’anga.

Nkhani ili mkamwa adatulukira Shati Choyamba.

“Mkulu iwe, ulipo? Kodi paja unkafuna kupha gogo wina ndi cholembera, zikuyenda bwanji? Nanga paja udalamulira pano pa Wenela nthawi ija gogo wathu akudwala, ndalama za penshoni udatani nazo?” adafunsa Abiti Patuma.

“Usandiseke. Maluzi andikwapula. Ana anga sakundithandiza mokwanira. Chonde pano pa Wenela musanyoze achikulire,” adayankha mkulu wa imvi zaphulusayo.

“Umufune! Kodi suja unkamuuza Mfumu Mose kuti sungayendere galimoto yotchipa kuposa BMW X5? Si iwe, ndiyankhe,” adatero Abiti Patuma.

“Komatu muzimvetsetsa. Ndili kukhala mu boys quarter pafupi ndi damu la anamasupuni ku Chimwankhunda,” adatero mkulu uja.­­­­­

“Kodi ndalama za penshoni sudamange nyumba? Nanga zotsogolera kutsutsa mopusa? Nanga za mapesi unkationetsa zija? Ukakamba za nyumba, ija ili pafupi ndi mtsinje njira ya ku East Bank?” ndidafunsa.

Adandiyang’ana kenaka adati: “Ndalama za penshoni samangira nyumbatu paja!”

Gwira bango, upita madzi.

 

Related Articles

One Comment

  1. Tadeyo is my good column i dont dare to miss.. come sunday, i make sure i buy the copy just as my priority to see what tadeyo has brought us from wenela..
    olo mpando waukulu, moya pete, shati yayifupi onse amakonda tadeyo..
    Nagwira bango… madzi anganditenge!

Back to top button