Chichewa

‘Olandira makuponi pano mu 2016 sadzalandiranso’

Listen to this article

 

Boma lati kuyambira chaka chino, yemwe wapindula nawo mupologalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya Farm Input Subsidy Programme (Fisp) wadyapo gawo lake lotsiriza chifukwa chaka chamawa kunka mtsogolo

sadzapezekanso pamndandanda wa olandira makuponi.

Nduna ya zamalimidwe, ulimi wamthirira ndi chitukuko cha madzi, Allan Chiyembekeza, ndiye adalengeza izi pamsonkhano wa atolankhani kulikulu la undunawu mu mzinda wa Lilongwe Lachiwiri lapitali.

Iye adati boma lachita izi poona kuti anthu omwe amapindula mupologalamuyi ndi omweomwewo koma saonetsa kusintha kulikonse, zomwe zidachititsa maiko ndi nthambi zomwe zimathandizirapo m’pologalamuyi kugwa mphwayi.

Mwayi womaliza: Ogula feteleza ndi mbewu za sabuside chaka cha mawa  adzadzigulira okha
Mwayi womaliza: Ogula feteleza ndi mbewu za sabuside chaka cha mawa
adzadzigulira okha

“Pologalamuyi idayambitsidwa ndi cholinga chopatsa alimi poyambira kuti zikawayendera azidzidalira koma malipoti akusonyeza kuti anthu omweomwewo ndiwo amalandira makuponi chaka n’chaka popanda kuonetsa

kusintha kulikonse,” adatero Chiyembekeza.

Iye adati poona izi, boma laganiza kuti lipereke mwayi umodziumodzi kwa anthu oyenera thandizoli ndipo yemwe zimukanike azidzionera yekha zochita mtsogolo chifukwa mwayi upita kwa anthu ena.

“Pakalipano, tili ndi mndandanda wa alimi a chimanga okwana 4.2 miliyoni ndipo mwa amenewa, tasankhamo alimi 1.5 miliyoni omwe athandizike chaka chino koma asayembekezere kuti chaka chamawa adzapezekanso pamndandanda wa alimi olandira makuponi,” adatero Chiyembekeza.

Koma wapampando wa komiti ya zaulimi m’Nyumba ya Malamulo, Felix Jumbe, sakugwirizana ndi ganizoli ponena kuti kumeneku kukhala kuweta umphawi wadzawoneni m’dziko muno.

Potsirapo ndemanga pa zomwe Chiyembekeza adanena, Jumbe adati n’zosatheka anthu ovutikitsitsa kusintha n’kukhala odzidalira paokha chifukwa cha matumba awiri a feteleza ndi paketi imodzi ya mbewu chifukwa zosowa pamoyo ndi zambiri.

“Zimenezi n’kungofuna kunyeketsa Amalawi opsa kalewa. Zoona munthu angasinthe ndi matumba awiri a feteleza ndi paketi imodzi ya mbewu basi? Ngati akufuna apange ndondomeko yabwino adzapereke zipangizo zokwanira zoti mlimi akhozadi kuimirapo iwo akasiya kupereka thandizo,” adatero Jumbe.

Iye adati m’maiko ena monga Zambia, alimi ena adakwanitsa kuima paokha chifukwa boma lidawapatsa zipangizo zokwanira-matumba 8 mlimi mmodzi-moti pano adaleka kudalira boma.

Jumbe adati njira yomwe boma la Malawi limatsata mupologalamu ya sabuside ndi yongopeputsa alimi osati kutukula ulimi monga momwe maiko otukuka adachitira kwawo.

Naye mfumu yaikulu Kabudula ya ku Lilongwe idadandaula ndi ndondomekoyi yatsopanoyi ponena kuti zikakhala choncho ndiye kuti anthu ambiri azivutika ndi njala komanso umphawi.

“Alimi ambiri malo awo olima ndi ochepa kwambiri moti ngakhale akolole n’kugulitsa zonse sangadzakwanitsebe kugula feteleza ndi mmene udakwerera mtengomu. Thumba limodzi la feteleza ndi K23 000 pomwe la

chimanga ndi K5 000 kutanthauza kuti mlimi akuyenera kusunga matumba 5 a chimanga kuti adzagule thumba limodzi la feteleza.

“Nanga poti alimi ambiri amafuna matumba a feteleza 4 kapena kuposa apo ndiye kuti agulitse matumba angati a chimanga kuti aime paokha? Mwinanso pakhomopo pali ana angapo akufunika fizi, zovala ndi kudya,” adatero Kabudula.

Mwezi wathawu, akadaulo pankhani za kayendetsedwe ka chuma a Economics Association of Malawi (Ecama) adalangiza boma kuti pologalamu ya sabuside ikuyenera kutha kaamba koti imapsinja ndondomeko ya chuma (bajeti).

Ngakhale m’madera ambiri mvula yobzalira yagwa kale, katundu wa sabuside yemwe wafika kale m’misika yomwe idakhazikitsidwa kuti anthu azikagulira zipangizozi sakukwana theka la katundu yense yemwe akufunika mupologalamuyi.

Mu pologalamu ya chaka chino, boma lakonza feteleza wokwana matani 150 000 omwe yemwe agawidwe pakatimpakati wokulitsira ndi wobereketsera ndipo matani okwana 3 000 ndi a mbewu za mtundu wa nyemba, soya, khobwe, nandolo ndi mtedza.

China chomwe chasintha mu pologalmu ya chaka chino ndi mitengo yomwe alimi azigulira zipangizozi monga K3 500 thumba la fetereza, K1 500 mbewu yachimanga ndinso K500 mbewu za mtundu wa nyemba.

Mitengoyi ndiyokwererapo kuyerekeza ndi mitengo yammbuyomu ati pofuna kuchepetsa ndalama zomwe boma limaononga mupologalamuyi.

Nduna ya zachuma Goodall Gondwe adati boma limaononga ndalama zankhaninkhani mupologalamuyi motero lidaona kuti n’koyenera kuwonjezera ndalama yomwe alimi amaikapo mupologalamuyi.

Iye adatinso kusintha kayendetsedwe ka pologalamuyi kuli pamndandanda wa zomwe maiko othandiza dziko lino adapereka kuboma la Malawi ngati likufuna kuti thandizo la zachuma liyambirenso kubwera.n

Related Articles

Back to top button