Nkhani

Ophunzira apewe uchidakwa—Polisi

Listen to this article

 A polisi m’dziko muno achenjeza ophunzira kuti asiye uchidakwa popeza mchitidwewu ukuononga tsogolo lawo.

Wachiwiri kwa mkulu woona ubale wa apolisi ndi anthu m’dziko muno, Masauko Medi, walankhula izi ku kusukulu ya sekondale ya Soche Hill mumzinda wa Blantyre pomwe apolisi amalangiza ophunzirawa zakuipa kwa uchidakwa.

Medi adati apolisi apeza kuti uchidakwa ndi chimodzi mwa zoipa zomwe zawanda pakati pa achinyamata, kuphatikizapo zogwiririra komanso kudzipha.

“Tikufuna ophunzira ayambitse makalabu m’sukulu ndipo azikambirana zothetsa mchitidwewu.Chitsanzo pasukulu ino kalabu yotere ilipo kale.

“Nkhani zachitetezo zikuyenera kuyambira ngakhale m’sukulu,” adatero Medi.

Patsikulo ophunzira adafunsa mafunso osiyanasiyana kwa apolisi komanso akuluakulu ena achipatala omwe amafotokozera ophunzirawa momwe uchidakwa ungasokonezere moyo wawo.

Ndondomekoyi, yomwe ikuthandizidwa ndi kampani ya Alcohol Manufacturing Companies kudzera mu Bwenzi Group of Companies yachitika kale ku Dedza, Ntchisi ndi Balaka.

Bungweli lidapereka pafupifupi K4.5 miliyoni zogwirira ntchitoyi.

Related Articles

Back to top button
Translate »