Chichewa

Ophunzira asanu anjatidwa ku Nkhotakota

Listen to this article

 

Apolisi Lolemba adamanga ophunzira asanu a sukulu ziwiri za m’boma la Nkhotakota ndi kuwatsegulira mlandu wofuna kudzetsa chisokonezo.

Mneneri wa polisi m’bomalo, Williams Kaponda, adatsimikiza za kutsekera m’chitolokosi kwa ophunzira anayi a pasukulu yoyendetsedwa ndi mpingo wa Anglican ya Bishop Mtekateka Private ndi wina wa sukulu ya sekondale yoyendera ya Linga Community Day Secondary School.

arrest

Kaponda adati mwa anayi amene adanjatidwa kusukulu ya Bishop Mtekateka, mmodzi ndi mtsogoleri wa anyamata pasukuluyi (headboy) Morton Mzumara, wa zaka 19.

“Utsogoleri wa sukuluyi udachotsa headboy pamene iye amalankhula kwa ophunzira anzake za aphunzitsi amene adamuphwanyira iPad,” adatero Kaponda. “Malamulo a sukuluyi amakaniza mwana aliyense kubwera ndi foni ndipo ichi nchifukwa chake mphunzitsiyo adali ndi mphamvu zomuphwanyira foniyo.”

Iye adati kuchotsedwa kwa Mzumara kudabala ziwawa chifukwa mogwirizana, ophunzirawo adafuna akuluakulu a sukuluyi afotokozepo bwino.

Pamene timalemba nkhaniyi nkuti sukuluyi itatsekedwa ndipo malinga ndi Kaponda, ikuyembekezereka kutsekulidwa Lolemba lino pamene ophunzira aliyense wapemphedwa kukabwera ndi makolo ake.

Mkulu wa mgwirizano wa makolo ndi aphunzitsi wa Parents Teachers Association (PTA) Luka Matchiya, wati kafukufuku ali mkati kuti apeze zomwe zidaonongeka pamene ophunzirawo adayamba kuswa zinthu chifukwa cha kuchotsedwa kwa anzawowo.

Ophunzira amene anjatidwawa ndi Mzumara wa m’mudzi mwa Chinguluwe kwa T/A Kalonga m’boma la Salima, Brave Mbewe, 20, wa m’mudzi mwa Kamange kwa T/A Malengachanzi ndi Mwayi Kalozi, 19, wa m’mudzi mwa Matiki kwa Senior Chief Kanyenda m’boma la Nkhotakota.

Enawo sitiwatchula chifukwa ndi a zaka zosakwana 18. n

Related Articles

Back to top button