Osaiwala kuteteza mtedza ku chuku

Pamene mbewu ya mtedza yacha, katswiri wa mbewu za mtunduwu kwa Bvumbwe Richard Andasiki akuti alimi ateteze mbewuyi ku chuku pamene akukolola, kuyanika, kusenda komanso kusunga.

Malinga ndi katswiriyu, mtedza umachita chuku mlimi akafulumira kapena kuchedwa kukolola, ukanyowa poyanika, mlimi akauviika m’madzi ndi cholinga choti asende mosavuta kapena akasunga pachinyontho.

Mtedza wopanda chuku umayenda malonda

“Tisaiwale kuti tikapitiriza kukhala ndi mtedza wa chuku sitingakhale ndi mwayi wogulitsa ku maiko akunja choncho miyoyo yathu komanso dziko lathu silingatukuke.

“Chinthu china chomwe chikuyenera kutipatsa mantha n’choti chuku chimatulutsa poizoni yemwe amayambitsa matenda a khansa ndi kunyentchera,” iye adatero.

Kuonjezera apo, mphunzitsi wa ku nthambi ya za ulangizi wa mbewu ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar), Paul Fatch adati poizoniyu amachepetsa chitetezo cha m’thupi komanso chilakolako cha zakudya.

“Poizoniyu akachuluka m’thupi, amachepetsa mphamvu yobereka,” adatero Fatch.

Pofuna kupewa zonsezi, Andasiki adati choyambirira alimi akolole mtedza wokhwima bwino, akaukumba awuyang’anitse kumwamba kufikira utauma ndipo akachoka apo, athothole ndikuuika m’matumba ndikusunga pouma.

Katswiriyu adafotokoza kuti mlimi akolole mtedza akaona kuti m’kati mwake makoko achita madontho akuda.

Pofuna kutsimikiza izi, iye adati mlimi akuyenera kukumba mapando okwana 10 mwapatalipatali ndipo akamaliza, athothole mtedza ochepa pa phando lililonse ndikuwusenda.

“Mlimi akapeza kuti mwa mtedza 100 omwe waswa, wosachepera 80 makoko ake ali ndi madonthowa ndiyekuti wakhwima ndipo ayambe kukumba,” adafotokoza motero.

Iye adati pamene mlimi akukumba mtedza akuyenera kuwuzonditsa kuti uyang’ane kumwamba ndi cholinga choti uwume bwino ndi dzuwa.

Mlangizi wa za ulimi wa mbewu ku Dowa Sangayemwe Kausiwa adati alimi akuyenera kusamala pokumba kuti wambiri usasalire m’munda.

Poyambirira, iye adati mlimi apewe kudzula mtedza koma azigwiritsa ntchito khasu.

“Pokumba, mlimi aziima pakati pa mzere ndikukuma mbali zonse ziwiri mwa mphamvu ndi cholinga choti onse unyamuke bwino,” adatero Kausiwa.

Mlangiziyu adati kuyenda m’munda ndikumatolera osalira kumathandizira kuti pafupifupi mtedza wonse uchokemo.

Iye adaonjeza kuti alimi apewe kuviika mtedza m’madzi kuti usavute kuswa chifukwa izi zimakolezera chuku.

Andasiki adafotokoza kuti alimi apewe kusunga mtedza wosenda kwa nthawi yaitali chifukwa umaonongeka.

“Malo wosungira mbewuyi akhale ouma komanso alimi ayiteteze ku makoswe,” adatero katswiriyu.

Moses Tanazio wa m’boma la Ntcheu ndi mmodzi mwa alimi omwe amatsatira bwino kwambiri malangizo pa ulimi wa mbewuyi.

Iye adati padakali pano sadayambe kukolola kufikira ukwaniritse zomwe alangizi adamuuza.

“Mtedza wanga ukakhwima, ndimakumba ndikuuyanika m’munda momwemo powuzondotsa  ndipo ndimathothola pokhapokha ukauma bwino.

“Mtedza owuma bwino umachita phokoso ukamautafuna choncho ukafika apa, ndimathothola, kuusankha, kuulongeza m’matumba abwino ndikuunga,” iye adatero.

Mlimiyu adati kuyanikiratu mbewuyi m’munda kumamuthandiza kuti akakafika nawo kunyumba asakavutike ndikuyanika. n

Share This Post