Nkhani

Ozunza mwana avomera mlandu

Bwalo la milandu ku Balaka lati pa 18 July lidzapereka chilango kwa mayi Lilian Matako omwe Lachisanu adavomera mlandu woti adazunza mwana wawo wamkazi pomumangirira ku mtengo atavomera kuti adaba K2 000 yawo.

Kanema wa mwanayo akulira ndi ululu atamangiriridwa mumtengo adafala m’masamba a mchezo ndipo mayiwo adawamanga powaganizira kuti adathiranso mwanayo madzi osakaniza ndi chitedze. Apolisi adamanga a Ishmael ndi Zuberi Chitete powaganizira kuti adachita nawo nkhanzazo.

Mayi Matako (Kumanja) ndi a Zuberi kulowa m’bwalo Lachisanu

Mneneri wa polisi ya Balaka a Gladson M’bumpha, adati bwalo litalowa Lachisanu, a Matako ndi a Ishmael adauvomera mlanduwo pomwe a Zuberi adaukana.

“Apa woweruza a Joshua Nkhono ati adzapereka chilango pa 18 July kwa amene mlanduwo auvomera. Koma mlandu wa amene aukana udzalowanso m’bwalo pa 16 July pomwe boma lidzabweretse mboni,” atero a M’bumpha.

A M’bumpha ati atatuwo akuwaganizira kuti adaphwanya gawo 235 ndime (b) ya malamulo a zilango m’dziko muno yomwe imaletsa kuvulaza ena modetsa nkhawa.Mwanayo ndi wa zaka 9 ndipo ali mu Sitandade 3 pa sukulu ya pulaimale ya Ngwangwa ndipo izi zidachitika pa 28 June m’mudzi mwawo.

Mayiyo adamenya mwanayo chifukwa adasolola K2 000 imene adasunga m’nyumba yawo akulowera m’tauni.

Apa mayiyo, mothandizana ndi anyamata ena adamangirira mwanayo n’kukmukapiza mwanayo madzi osakaniza chitedze.

A Matako, omwe amachokera m’mudzi mwa Kanyumbaka kwa T/A Sawali m’bomalo akaonekera ku khoti posachedwapa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button