Nkhani

Pulezidenti asamale ndi atidye nawo

Mafumu, mphunzitsi wandale kusukulu ya ukachenjede ku Chancellor College kudzanso Amalawi ena ati mchitidwe wa andale ena posintha zipani kuti alowe chipani cholamula—chonsecho maliro a mtsogoleri wakale ali m’nyumba—ungosonyeza kuti ndi anthu a dyera.

Akuluakuluwa ati ichi ndi chisonyezo kuti aphungu kapena nduna zina sizifuna kutukula Amalawi koma kusakaza zomwe zimayenera kuti zitukule anthu akumudzi.

Akuluakuluwa ati kotero pomwe chipani cha People’s (PP) chikulandira aphungu osomphoka kwina chisamale maka a chipani chakale cholamula cha DPP akhale tcheru ndi amadyowo.

Ndemangazi zikudza kutsatira imfa yadzidzi ya mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bingu wa Mutharika yemwe adamwalira Lachinayi pa 5 mwezi uno atadwala matenda a mtima.

Zitadziwika kuti a Bingu atisiya, yemwe adali wachiwiri wawo, Joyce Banda, adalumbiritsidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino potsatira malamulo a dziko la Malawi.

Msamuko

Koma Banda asadalumbiritsidwe n’komwe, aphungu komanso nduna zina zidaneneratu kuti izo zilowa chipani cha PP, ati potsatira zomwe anthu awo awauza.

Nduna komanso aphungu ena akuti akhala akufika komwe kukukhala Banda kapena kuwailesi ya MBC kukalengeza kuti zalowa chipani cha Banda.

Mwa ena, monga nduna ya zantchito, Lucious Kanyumba ndi wachiwiri kwa pulezidenti wa chipani cha DPP, Yunus Mussa adanenetsa kuti iwo tsono alowa chipani cha Banda ati anthu omwe adawasankha ndiwo anena.

Apa ounikira ati ili ndi dyera chifukwa pachikhalidwe simuyenera kukamba nkhani zina pomwe maliro adakali m’nyumba.

Iwo achenjezanso kuti Banda akuyenera kusamala ndi atidyenawo chifukwa atha kudzathawanso ngati chipanichi sichikulamula.

T/A Kapeni ya m’boma la Blantyre yati pofika Lachitatu idali isadalumikizane ndi phungu wake kumeneko. Koma iyo adati pamiyambo ya makolo sikololedwa kumakamba nkhani zina maliro ali m’nyumba.

“Pakhomo pakagwa azimu timadikira kuti tiike thupiro ndiye timakhala omasuka kukamba zina zokonza kapena kungounikira kumene.

“Tikamamva kuti zimenezi zayamba kale kuchitika zikutimvetsa chisoni; sibwino nthawi ino kukamba zoterezi. Ichi sichingakhale chitukuko chikunenedwacho, akuyenera kudikira mpaka titaika maliro,” idatero mfumuyi.

Aphungu adyera

 

T/A Kachindamoto ya m’boma la Dedza yati aphungu akumangonama kuti akutsata zomwe anthu omwe adawaika pampando anena.

“Ife phungu wathu kuno sadabwere kudzatifunsa maganizo ake ndipo sitingalolenso kuti tiyambe kukamba zimenezi maliro ali m’nyumba.

“Umu simmene pachikalidwe chathu zikhalira. Tidikire kuti tikaike wokondedwa wathu bwinobwino monga a Pulezidenti anenera,” adatero Kachindamoto.

Senior Chief Malemia ya m’boma la Nsanje yati phungu wawo yemwenso ndi wachiwiri kwa nduna ya zamigodi, Vera Chelewani adaitanitsa mafumuwo ndikuwafunsa chomwe iye ngati phungu wawo ayenera kuchita.

Malemia wati zomwe adauza ndunayi n’kuti igwire ntchito ndi boma chifukwa boma ndilo limaitanitsa chitukuko kumidzi monga kumanga mijigo ndi milatho komanso sukulu.

“Kaya akalowa chipani kaya ayi ife chomwe tikufuna n’kuti agwire ntchito ndi boma kuti chitukuko chitifike.

“Ife mafumu tilibe chipani; chomwe tichita n’kuthandiza boma lolamula kuti ligwire bwino ntchito yake.

“Zambiri sizili bwino m’dziko muno monga kusowa kwa ndalama zakunja komanso mafuta,” idatero mfumuyi.

Iyo idati sidakambe zambiri ndi phunguyo ponena kuti sikulondola kukamba zambiri chikhalirecho maliro ali m’nyumba.

Sadatifunse

 

Mlimi wa mtedza ndi chimanga, Nellie Banda wa m’mudzi mwa Champiti kwa T/A Champiti m’boma la Ntcheu wati phungu wawo kumeneko yemwe ndi wachiwiri kwa sipikala wa nyumba ya Malamulo, Jones Chingola, sadawafunsepo za ganizo losintha mawanga.

“Kuno tili ndi mavuto a kusowa sukulu, milatho koma phunguyu palibe chomwe wachita ndiye akamati akufuna chitukuko akutanthauza chani?

Martin Susuwere wa m’mudzi mwa Godeni kwa T/A Mpama m’boma la Chiradzulu wati phungu wawo kumeneko yemwenso ndi nduna ya maboma ang’ono, Henry Mussa sadafikenso kuti amve maganizo awo.

“Abwere adzatifunse maganizo athu,” adatero dilaivalayu.

Apa Chunga watsendera kuti aphungu kapena nduna zobulika ku zipani zawo lero zilibe mtima wofuna kutukula dziko kapena kuthandiza omwe adazisankha.

Iye wati nduna zina zakhala zikuchita chimodzimodzi kuchokera kuchipani cha MCP, UDF ndi DPP ndipo pano zikufunanso zichite chimodzimodzi pomwe zikufuna zilowe ku PP.

Banda asakomedwe

 

Chunga wati ngakhale aliyense ali ndi ufulu wolowa chipani chomwe wafuna, komabe Banda asakomedwe ndi anthu oterewa ndipo sikoyeneranso kuwapatsa maundindo.

Kastswiriyu adatsendera zonse ndi kuyamikira kusintha komwe Banda adachita pamaunduna ena.

Lachiwiri m’sabatayi, Banda adasintha unduna wofalitsa nkhani omwe udapita kwa Moses Kunkuyu yemwe adalowa m’malo mwa Patricia Kaliati.

Iye adasinthanso mkulu wa nyumba yowulutsira mawu ya boma ya MBC pomwe adachotsa Bright Malopa n’kuika Benson Tembo komanso kuchotsa yemwe adali mkulu wa apolisi, Peter Mukhito ndikuika Loti Dzonzi.

Iye adasinthanso mlembi wamkulu muunduna womwe umayendetsa chuma cha boma, Joseph Mwanamvekha n’kuikapo Radson Mwadiwa yemwe adalinso paudindowu mu 2009.

Banda wachenjeza kuti onse omwe akufuna kulowa chipanichi asapite pawailesi koma akumane ndi mlembi wachipanichi.

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.