Ras Chikomeni sizidamukomere

Pofika Lachisanu Ras Chikomeni Chirwa adali yakaliyakali kusakasaka K2 miliyoni kuti akapereke ku bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC).

Izi zimadza pamene bungwelo lidabweza Chirwa ponena kuti adali asadapereke ndalamayo komanso adali asadasayinitse m’maboma 9 chomwe ndi chomuyenereza china.

Chikomeni ndi mayi ake akuti alibe chilichonse

Komabe Chirwa adati siwokondwa ndi zomwe MEC idachita chifukwa zidaonetsa kuti anthu olemera okha ndi amene akuyenera kuimira ngati pulezidenti wa dziko.

“Ndinabwera kudzaonetsa ufulu wanga koma akundikana chifukwa ndine wosauka. Sindingakwanitse kupeza ndalama imeneyo ndiye poti ndine wosauka andikanira,” adatero Chirwa.

Izi zidachititsa kuti bungwe la Centre for Human Rights Education Advice and Assistance (Chreaa) lilowere kubwalo lamilandu kukatenga  chiletso kuti MEC ilandire mapepala a Chirwa.

Mkulu wa Chreaa Chikondi Chijozi adati K2 miliyoni n’chimodzimodzi kukaniza chirwa kuti asapikisane nawo pa mpando wa pulezidenti.

“Ndalama zachuluka ndipo uku ndikuletsa anthu osauka kuti asapikisane nawo koma olemera okha,” adatero Chijozi.

Lachisanu kudalinso zoseketsa pamene MEC idabwezanso Smart Swira wochokera m’boma la Chitipa amene amafuna kupikisana nawo.

Swira atafika ku holo ya Comesa adaseketsa anthu chifukwa adalibe wachiwiri wake ndipo amati wathamangira kuchipatala ndi mwana amene amati akudwala.

Koma mkulu wa MEC Jane Ansah adakana kulandira makalata a Swira ponena kuti sadalembetse m’kaundula wa zisankho, komanso alibe chizindikiro kuti ndi M’malawi.

Swira adati pachipanda MEC kumubweza “bwezi atakwapula onse [amene akupikisana nawo pa mpandopo.”

Wina amene adamubweza ndi Damiano Ganiza woipa payekha chifukwa adalibe zomuyenereza n

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.