Nkhani

Shasha si wamankhwala

Listen to this article

Zonga sewero zidachitika pa Kamuzu Stadium pamene Nyerere zidakokera kuuna Shasha pomukayikira kuti ndi wa timu ina yemwe amafuna achite chidima timu yawo.

Tikukambamu timuyi yalembera bungwe la Sulom kuti Shasha asamakhalenso pamasewero awo ponena kuti akufuna wovala Shasha azikhala wa timu yawo.

Nyerere zikuganiza kuti amene akumavala Shasha ndi wosapotera matimu ena ndipo akufuna awavulaze osati kukhazikitsa bata.

Ife aganyu nkhaniyi tilibe nayo vuto, kulemekeza ganizo la Nyerere tikukhulupirira kuti sikulakwitsa, komabe tili ndi mafunso.

Kodi Nyerere zikukhulupirira kuti Shasha angapangitse kuti asamapambane magemu? Ngati nzoona, bwanji Nyerere zidaluza masewero awo ndi Silver Strikers pa Kamuzu Stadium m’chikho cha Standard Bank, ngati vuto ndi Shasha?

Tikudabwa chifukwa Shasha amapezeka m’ligi mokha ndipo gemu yawo ndi Silver Shasha kudalibe chifukwa udali mpikisano wina. Adaluza bwanji poti kudalibe Shasha?

Kodi Nyerere zikukhulupirira kuti mankhwala angagwire ntchito mumpira? Ngati amagwira ntchito, bwanji sakupanga mankhwala kuti asulutse zomwe Shasha wawachita?

Posakhalitsapa kudabwera timu ya Benin m’dziko muno. Timuyoo idakana kukwera galimoto zomwe FAM idawakonzera komanso idakana kugona malo amene adaikonzera ponena kuti awachita mankhwala, koma bwerani masewero adagonjanso.

Mu 2009 kudabwera DR Congo yomwe idabweretsa mbiya zamankhwala ndipo amafukiza pa Kamuzu Stadium, koma adagonja 2-1. Ndiye mankhwala amagwiradi ntchito?

Nyerere bwanji zikambe nkhani ina chifukwa za juju ife sitikukhulupirira kuti zingawachititse kugonja.

Komanso mukati Shasha azikhala wa timu yanu, nanga mukamasewera ndi anzanu zizikhala bwanji? Kodi anzanuwonso sazifuna avale nawo?

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button