Sungani mbatata m’munda, M’nkhuti kuti isaonongeke


Alfred Mumba wa m’boma la Dowa  amalima mbatata pa malo okwana maekala 5.

Iye amapeza matumba osachepera 250 a mbatata pachaka kuchokera pa malowa koma chomvetsa chisoni n’choti amangokwanitsa kugulitsa theka lokha la zokolola zake.

Mbatata imasungika nthawi yaitali mukaisamala bwino

“Ndikanyamula matumba 10 kupita nawo ku msika, 5 okha ndiomwe ndimagulitsa pa mtengo  wabwinoko ndipo osalawo, ndimagulitsa mongotaya kapena kungozisiya ku msika komweko.

“Izi zimakhala chomwechi chifukwa ogulawo amatiphwathulitsa matumba ndikusankhamo zomwe akufuna ndipo zotsalazo amazisiya ndikupita kwa ogulitsa wina,” iye adatero.

Katswiri wa mbewu za mtunduwu kwa Bvumbwe Miswell Chitete adati zokolola za mbewuyi za pakati pa 30 ndi 50 pa 100 zilizonse zimaonongeka m’dziko muno.

Iye adati ngakhale mbatata  sizichedwa kuonongeka, zimakhala osaonongeka mosachepera miyezi itatu zikasiyidwa m’munda momwemo osazikumba kapena miyezi 9  zikasungidwa m’nkhuti.

Malinga ndi Chitete, njirazi ndizothandiza kuti mlimi azitha kugulitsa mbewuyi pang’onopang’ono kapena nthawi yomwe yayamba kusowa choncho akhoza kupindula nayo.

“Mbatata ikakhwima sizikutanthauza kuti mlimi akolole yonse ndikupita nayo ku msika chifukwa akagulitsa yochepa chabe ndipo yambiri izangoonongeka kapena agulitsa mongotaya,” iye adatero.

Iye adafotokoza kuti mlimi akhoza kuilekerera m’munda momwemo ndikuzayamba kukumba pamene waona kuti mbatata yachepa pa msika kuti apindule nayo kwambiri.

Katswiriyu adati vuto lomwe mlimi akhoza kukumana nalo posunga m’munda ndi la kufumbwa kwa mbatata kaamba ka anankafumbwe.

Chitete adati vutoli  silalikulu kwenikweni chifukwa akhoza kuthana nalo pokwirira ming’alu kuti anankafumbwewa azisowa polowera.

“Mlimi akhoza kusankha kusunga mbatata yake mu nkhuti ndikuzaigwiritsa ntchito m’tsogolo kapena kumatengamo pang’onopang’ono kufikira izathe,” iye adatero.

Katswiriyu adati nkhuti ndi dzenje losungiramo mbatata ndipo mlimi amakumba molingana ndi kuchuluka kwa zokolola zake za mbewuyi.

Akamaliza kukumba, Chitete adati mlimi amayenera kusanja mbatata yake m’zigawo.

Iye adafotokoza kuti pamwamba pa chigawo chilichonse amayenera kuwazapo phulutsa kapena mchenga ndipo dzenje lija likadzadza, alikwirire.

Akachoka apo, katswiriyu adafotokoza kuti mlimi amayenera aziyifukula mwezi uliwonse n’cholinga choti akapeza kuti ikumera, azichotsa mphukirazo ndipo potero imasungika kwa nthawi yaitali.

“Njira ina yotetezera mbatata kuti isaonongeke ndikuipala makaka.

“Makakawa akauma mlimi akhoza kupanga ufa ndikumaphikira phalala, thobwa ndi zina zambiri,” iye adatero.

Katswiri wa mbewu za  masamba ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) Eric Chilembwe adati alimi akhoza kuchulukitsa phindu ku mbewuyi pogulitsa yophika kale kapena yootcha.

“Mulu umodzi wa mbatata umagulitsidwa motsika mtengo pamene kuyiphika kapena  kuyiotcha ndikumagulitsa ndalama yake imakhala yooneka,” iye adatero.

Jean Pakuku ndi m’modzi mwa anthu a bizinesi omwe akupititsa patsogolo miyoyo ya alimi m’dziko muno powagula mbatata yofiyira m’kati ndikumapangira zinthu monga buledi ndi masikono.

“Ndidaona maiko ena muno mu Africa mbatata siyionongeka chifukwa amayigwiritsa ntchito kupangira zinthu zosiyanasiyana choncho tikhoza kuchita chimodzimodzi m’dziko mwathu muno,” iye adatero.  n

Share This Post