Nkhani

Thalaveni isanduka powerengera mabuku

Anthu omwe amapita kukaziziritsa kukhosi ndi mowa wa Chibuku ku Zingwangwa mumzinda wa Blantyre ayiwale pomwe kampani ya Chibuku Products Limited (CPL) yapereka yomwe kale ankamweramo mowa wa Napolo ku bungwe la Young Achievers for Development (YAD).

Bungweli lomwe limathana ndi nkhaza za m’banja komanso kupititsa patsogolo maphunziro pakati pa achinyamata lisandutsa nyumbayo kuti ikhale malo owerengeramo komanso ofesi ya chinsinsi.

Mkulu wa YAD, Jefferson Milanzie wati nyumbayo yomwe idzitchedwa ‘Tingathe Community Multipurpose Resource Centre’ ithandiza dera la Zingwangwa komanso madera ozungulira pomwe akhale ndi malo okawerengerako.

Iye adati bungwe lawo lidakambirana ndi kampani ya Chibuku kuti awathandize ndi malo ndipo pa 3 Ogasiti chaka chino, kampaniyo idapereka nyumbayo pamwambo omwe udachitikira ku hotelo ya Sunbird Mount Soche mumzindawu.

Loweruka pa 22 Sepitembala kudali mwambo wotsegulira malowo kuti ayambe kukonzedwa.

“Tikuyembekezera kugwiritsa ntchito K13 miliyoni kuti tikonze malowa. Kudzera mu m’sonkhemsonkhe, takwanitsa kugula malata, mchenga ndi njerwa 5 000,” adatero Milanzie.

Iye adati bungwelo lalandira thandizo kuchokera ku Famers World, Kriss Offset and Screen Printers ndi PG Glass.

Mmodzi mwa akuluakulu a kampani ya Chibuku, Wise Chauluka yemwe adali pamwambowo adati bungwe lawo lidakhutira ndi ntchito za YAD kotero adapeza kuti ndikothandiza kupereka nyumbayo ku bungwelo.

Related Articles

Back to top button