Thambo lagwa kwa Bvumbwe

Listen to this article

Thambo lagwa! Yagona ngwenyama, mfumu Yachingoni kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo, komwe anthu ochokera m’maboma osiyanasiyana akhamukire m’mudzi mwa Makungwa kukaperekeza thupi la Inkosi Bvumbwe, yomwe idagona Lachitatu lapitali.

Mneneri mu unduna wa maboma aang’ono Muhlabase Mughogho adatsimikizira za imfa ya Bvumbwe ponena kuti adatsamira mkono atadwala kwa kanthawi kochepa kuchipatala cha Blantyre Adventist.

Alowa m’manda leweluka: Bvumbwe
Alowa m’manda leweluka: Bvumbwe

T/A Bvumbwe adadziwika kwambiri kaamba ka kulimba mtima kwake mu May 2013 pamene adadzudzula chipani cha PP pogawa nsalu za chipani patsiku la maliro a jaji Joseph Manyungwa.

Iye adadzudzula chipanichi mtsogoleri wake Joyce Banda, yemwe panthawiyo adali pulezidenti wa dziko la Malawi, ali pomwepo. Izi sizidakondweretse mtsogoleriyu komanso chipani chake ndipo adakakamiza Bvumbwe kuti apepese, apo bii amuvula ufumu.

Inkosi Bvumbwe, yemwe dzina lake adali Christopher Bvumbwe, idali mfumu yachisanu kuvala ufumuwu ndipo ufumu wake adautenga kuchokera kwa bambo ake, Steven Bvumbwe, yemwe adamwalira pa 3 June 2001.

Mfumuyi idakhala pampando ili ndi zaka 23 malemu bambo ake asakupeza bwino chifukwa cha matenda a kuthamanga kwa magazi.

Bvumbwe atamaliza sekondale ya Luchenza mu 1998, adapita ku Mzuzu komwe adayambako kuchita kozi ya Business Administration ku Golden Age Professional College.

Adangophunzirako kwa mwezi umodzi pamene adaitanidwa kuti abwere kumudzi chifukwa cha kudwala kwa bambo ake mu 1999.

Mosakhalitsa bambo ake adagona ndipo mu November 2001 adalongedwa kukhala T/A Bvumbe Yachisanu ndipo mtsogoleri wa dziko lino panthawiyo, Bakili Muluzi, ndiye adalonga mfumuyi yomwe idali yachitatu kubadwa m’banja la ana 6.

Ngakhale ufumu wake wakhala ukugwedezeka ndi banja la Mphedzu la m’boma la Thyolo ponena kuti iwo ndi eni ufumuwu, Bvumbwe wakhala akutsogolera anthu ake pankhani zachitukuko ndipo mu 2013, Inkosi ya Mamakhosi Gomani V idapereka mphotho kwa mfumuyi pochita bwino pankhani za chitukuko.

“Panthawiyo ndimayendera mafumu anga momwe akuchitira pankhani ya chitukuko. Pamafumu onse, Bvumbwe ndiye adachita bwino kusiyana ndi ena ndipo adali nambala wani,” adatero Gomani.

Kodi Gomani akumva bwanji pamene mfumuyi yatsamira mkono?

“Eee! Ndine wolira chifukwa cha imfa imeneyi, mukudziwanso kuti adali mchimwene wanga. Ufumu wake udali wa Maseko, womwenso ndi ufumu wanga. Chifukwa cha ichi adali mchimwene ndithu.

“Ndadandaula kwambiri. Komanso m’boma la Thyolo, Bvumbwe ndiye amaimira mtundu wathu, monga mfumu Yachingoni,” adalira Gomani.

Bvumbwe woyamba, yemwe dzina lake adali Zulu, adamwalira mu 1926 ndipo ufumuwu udaperekedwa kwa Julius yemwenso adasiyira Mission asadapereke kwa mwana wake Steven.

Steven ndiye adapereka ufumu kwa Bvumbwe amene wagona leroyu, yemwe mayi ake amachokera kwa Inkosi Mwabulabo m’boma la Mzimba ndipo adamwalira pa 5 July 1996.

T/A Bvumbwe wamwalira ali ndi zaka 37 ndipo wasiya mkazi ndi ana awiri.

Related Articles

Back to top button