Tizipatsana ulemu moyendamu

Abambo ndi anyamata, pali makhalidwe ena omwe mukuyenera kusiya. Makhalidwe onyasa, otopetsa otonza amayi ndi atsikana.

Zomati muntu wamkazi akudutsa poteropo abambo ndi anyamata ena n’kumayang’ana mwachidwi chachipongwe ngati mukumusilira munthuyo, n’zoipa.

Amayi ndi atsikana ali ndi ufulu oyenda mosasowetsedwa mtendere ndi mayang’anidwe otero aja.

Ndiye pali miluzi ija m’malizaliza, kulizira amayiwa kaya anzanu pofuna kuti nawo achite chidwi ndi mayi kaya mtsikana amene akudutsa.

Ena ndi aja simutha kuugwira mtima koma mpaka mkono wanu ugwire mtsikana kaya mayi mosamulemekeza.

Palinso timamoni tosadziwika bwino tija m’mapereka mmisewumu. Ena m’makhala kumachemerera kapena kunyoza ziwalo za amayi ndi atsikana akamadutsa.

N’chifukwa chiyani simutha kupita pagulu la anthu n’kungosamala za inu nokha osalabadirako za anthu ena?

Chimavuta n’chiyani kuona munthu wa mayi, n’kumupatsa ulemu omwe m’mapatsa abambo ndi anyamata anzanu? Chifukwatu miluziyi, mamoni, kugwirana ndi zinazi simupangira abambo anzanu.

Ndithu m’maganiza kuti munthu wamayi amanka m’liyendamu kuti inu mumugwire, kapena kumukuwa kaya kumuyankhulitsa zosadziwika bwino?

Chimakupatsani danga loti muzisowetsa amayi mtendere n’chiyani?

Ili ndi khalidwe lonyasa lochokera m’maganizidwe aja oonera amayi ndi atsikana pansi, kumawayesa ngati anthu omwe mukhoza kuwazunguza mmene mungaganizire.

Mungamve bwanji bambo kapena mnyamata wina atagwira bere la mayi wanu?

Mungamve bwanji wina atamayimbira miluzu kusowetsa mtendere mkazi wanu?

Mungamve bwanji wina atamachonga ziwalo za mchemwali wanu kapena mwana wanu wa mkazi?

Share This Post