Chichewa

Uve ndi gwero la linyonyo

Listen to this article

Mkulu wa bungwe la Heart to Heart Foundation(HHF) m’boma la Machinga Derlings Phiri wati gwero  la matenda a linyonyo ndi uve.

Malingana ndi Phiri, linyonyo ndi matenda a maso omwe munthu akalekerera kwa nthawi yaitali amayambitsa  khungu.

Kusamba kumaso ndi sopo kumathandiza kupewa linyonyo

Iye adafotokoza kuti kukanda kapena kugwira m’maso ndi m’manja mosatsamba kumaika  maso  pa chiopsezo cha linyonyo chifukwa m’manja mwa uve mumakhala tizilombo ting’onoting’ono toyambitsa matendawa.

“Ndi bwino kuti nthawi zonse anthu azisamba m’manja ndi sopo akachoka ku chimbudzi, akamaliza kusintha ana matewera komanso akagwira chinthu china chilichonse asanagwire m’maso mwao,” adatero Phiri.

Mkuluyu adati  anthu akaona zizindikiro za matendawa monga kutuluka misonzi pafupipafupi, kuyabwa, kufiira maso ndi zizindikiro zina azithamangira ku chipatala kuti akapimidwe ndi madotolo.

“Osathira mankhwala a  zitsamba m’maso chifukwa  zina  zimakhala dziphe zomwe zikhoza kuononga maso,” adatero mkuluyu.

Phiri adati ngakhale  linyonyo  limagwira munthu wina aliyense, limayala maziko kwambiri pa ana.

Iye adati izi zimakhala chomwechi chifukwa ana nthawi zambiri amasewera pa fumbi ndi malo ena omwe amakhala ndi tizilombo toyambitsa matendawa makamaka ngati sakumbukira kusamba m’manja asadakande m’maso.

“Ndi udindo wa makolo kuphunzitsa  ana  kuti azikupewa kukanda m’maso ndi m’manja mwa uve kuti linyonyo litheretu m’dziko muno,” adatero mkuluyu.

Phiri adaphera mphongo potsindika kuti munthu wina aliyense azisamba kumaso ndi sopo akangozuka  chifukwa manthongo amaitana  tizilombo toyambitsa linyonyo.

Related Articles

Back to top button
Translate »