Voti yotengera zigawo ilipobe

Amalawi akadali ndi mtima wovota potengera chigawo chomwe amachokera ndi munthu kapena chipani chomwe akulumikizana nacho m’njira inayake makamaka mtundu.

Mwachitsanzo, pa zisankho ziwiri zapitazi za 2014 ndi 2019, chipani cha DPP chakhala chikupeza ma voti ambiri ku mmwera, MCP m’chigawo chapakati pomwe kumpoto kudavotera kwambiri zipani za UTM and PP.

Duwa: Anthu ali kale ndi mbale

Zotsatira za chisankho cha chaka chino zawonetsa kuti kavotedwe ka anthu sikadasinthe kwenikweni ndipo zangokhala ngati mkopera wa zotsatira za chisankho cha 2014 makamaka kwa zipani za MCP

ndi DPP zomwe zimapikisana kwambiri.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi zisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa wati izi zili choncho chifukwa anthu saphunzitsidwa mokwanira za momwe angasankhire atsogoleri komanso zipani za ndale zimalephera kutambasula mfundo zake kuti anthu asinthe maganizo pambali yovotera.

“Anthu ali kale ndi mbali potengera zigawo zochokera chifukwa aliyense amafuna kukokera kwake koma malingaliro oterewa akhonza kusintha potengera momwe anthu aphunzitsidwira pa kasankhidwe ka atsogoleri komanso momwe zipani zatambasulira mfundo zake,” adatero Duwa.

Katswiri pa ndale Ernest Thindwa adati kuvota kwa malingaliro otere kawirikawiri kumachititsa kuti mtsogoleri azisankhidwa ndi anthu ochepa zomwe ngakhale zimaloledwa m’dziko muno potengera malamulo achisankho, n’zosayenera mu demokalase.

“Demokalase imatanthauza kuti anthu azisankha mtsogoleri yemwe akufuna ndipo azisankhidwa ndi anthu ambiri. Mwachidule, opitirira theka la anthu onse omwe adaponya voti ndiye kuti demokalase ikuyenda,” adatero Thindwa.

Share This Post