Chichewa

Wa zaka 18 akaseweza zaka 18

Listen to this article

Bwalo lamilandu mumzinda wa Mzuzu lagamula Mulolo Nkhata wa zaka 18 kukakhala kundende zaka 18 atamupeza wolakwa pamlandu wogonana ndi mwana wa zaka 6.
Zidamveka m’bwalolo kuti mnyamatayo ankagwira maganyu kunyumba kwa makolo a mwana ochitidwa chipongweyo ndipo kaamba ka kubwerabwera kwake pakhomopo adayamba kudziwana ndi yo.
Nkhata ndi wochokera m’mudzi mwa Chikwina T/A Nyalubanga m’boma la Nkhata Bay.
Mneneri wa polisi mumzinda wa Mzuzu Patrick Saulosi adati Nkhata adavomera kulakwa kwake pamlanduwo.

arrest
Iye adati woimira boma pamlanduwu, sub-inspector Lyson Kachikondo, adapempha bwalo lamilandu kuti chigamulo chikhale chokhwima kaamba kakuti mlanduwu ndiwaukulu komanso zomwe wamudutsitsa mwanayo ndi chinthu chomwe sangadzaiwale moyo wake onse.
“Ogamula mlanduwu, Tedious Masoamphambe adavomereza zomwe adanena Kachikondo ndipo adati chigamulo chachikulu chithandiza kuchepetsa kuchuluka kwa milandu ya ntunduwu,” adatero Saulosi.
Izi zili choncho bambo wa zaka 47, Wilson Nyirenda, wa m’boma la Nkhata Bay wagamulidwa kukhala ku ndende zaka 14 atagonana ndi mwana wa zaka 12.
Mneneri wa polisi wa m’boma la Nkhata Bay Ignatius Esau adati mwezi wa August, Nyirenda yemwe ndi wochokera m’mudzi mwa Chikalanda T/A Chikulamayembe ku Rumphi adamuitanira mwanayo mu nyumba mwake momwe adamugwiririra.
“Mwanayo adatuluka m’nyumbamo akulira zomwe zidachititsa anthu kuti amufunse zomwe zamuchitikira ndipo mwanayo adaulula,” adatero Esau.
Iye adati Nyirenda adakana mulanduwo koma adapezeka wolakwa anthu anayi atachitira umboni za nkhaniyi.
“Iye adati anthu ankamunamizira chifukwa amachita naye nsanje poti siochokera m’mudzimo. Adauzanso bwalolo kuti adali ndi matenda a chinzonono ndipo adauza makolo a mwanayo kuti apite naye kuchipatala. Adapitiriza kuti adakhala nthawi yaitali asadagonane ndi mkazi ndipo ‘ngati
adagwiririradi mwanayo’ ndiye kuti adampatsa mimba,” adatero Esau.
Iye adati ogamula mlanduwu, Billy Ngosi, adati milandu yogwiririra ikukula ndipo olakwa akuyenera kupatsidwa chigamulo chonkhwima kuti chikhale chiletso kwa ena.

 

Related Articles

Back to top button