Wogwiririra n’kupha mwana agwidwa

Apolisi m’boma la Mchinji apulumutsa bambo wina Boyd Sakala wazaka 33 anthu a m’mudzi mwa Nkhomba kwa T/A Zulu ku Mchinji akufuna kumupha pomuganizira kuti adagwiririra n’kupha mwana wake wompeza wa zaka zitatu.

Mneneri wapolisi ku Mchinji Lubrino Kaitano wati mkuluyu akumuganizira kuti adachita izi pa January 31 2019 mkazi wake atapita kumsika wa ku boma ku Mchinji kukagulitsa mango.

Adapulumukira m’kamwa mwa mbuzi: Sakala

Kaitano wati Sakala adakwatira Dorina Phiri wa zaka 35 m’chaka cha 2018 ndipo amakhala naye limodzi m’mudzi mwa Sankhani kwa T/A Mlonyeni m’bomalo ndipo adatenga mwana wompeza wa zaka zitatuyo kuti amulere.

“Mkazi wakeyo atapita kumsika, iye adapezapo mwayi wogwiririra mwanayo n’kumufinya pakhosi mpaka kupha ndipo anthu ena adamuona atanyamula saka akulowera kumunda,” watero Kaitano.

Iye wati mkazi uja pobwera kumsika, adapeza bamboyo ndi mwana yemwe palibe koma patatha nthawi pang’ono, bamboyo adatulukira yekha opanda mwana zomwe zidazunguza maiyo mpaka adayamba kufufuza m’mudzimo.

Iye wati atafufuza kwa kathawi osampeza

Iye wati auza komiti yoyang’anira za chikhalidwe pakati pa Achewa kuti apite m’mudzi mwa Chiyendera Mwano n’kukafufuza nkhaniyi ndipo wati ngati anyamatawo amachokera m’madera a mafumu a Achewa, mafumuwo alipitsidwa ng’ombe zopepesera Kalonga Gawa Undi.

Lukwa wati mafumuwo akhoza kupulumuka ngati ali pansi pa ufumu wa Chingoni chifukwa sadziwa mwambo wa Chichewa koma wati anawo akapezeka kuti ndi a m’dera la Chingoni, awaganizira kuti amayeserera gulewamkulu ndi zolinga zina monga kuchita zaupandu.

“Dera mukunenalo la Vusojere ndi la Chingoni koma nthumwi zipitabe kukafufuza. Zimatipweteka kuti anthu azikhalidwe zina aziyeserera gulewamkulu chifukwa ambiri amapangira zolinga za upandu osati chikhalidwe momwe timalemekezera eni akefe,” watero Lukwa.

Lamya za mafumu awiri omwe anyamatawo amachokera Kapondera ndi Chiyendera Mwano sizimapezeka pomwe timayesa kumva mbali zawo pankhaniyi.

Koma apolisi ati akusunga mnyamata wa zaka 12 yemwe akumuganizira mlandu wakuphawo.

Mkulu wa bungwe la Centre for Human Rights Education Advice and Assitance (Chreaa) Victor Mhango wati apolisi akuyenera

kutsimikiza kaye kuti mnyamatayo ankadziwa zomwe amapanga asadamutengere kukhothi kukamuzenga mlandu.

“Ndime 14 (2) ya malamulo imati munthu yemwe sadafike zaka 14 sayenera kuzengedwa mlandu pa zomwe wapanga pokhapokha patakhala umboni woti munthuyo amadziwa zomwe amapanga panthawiyo,” watero Mhango.

Iye wati kuonjezera apo, ndime 88 ya malamulo otetezera ndi kusamalira ana imati mwana sayenera kusungidwa pamalo omwe angapsinjike ku thupi, uzimu ndi maganizo ngati kundende.

Mhango wagwirizana ndi malamulo omwe adakhazikitsa Achewa kuti munthu aziloledwa kulowa gulewamkulu pokhapokha akadutsa zaka 18.

Anthu ochuluka akhala m’ndende nthawi yaitali kudikira milandu yawo yowaganizira kupha chifukwa boma limati pakadalibe ndalama zozengera milanduyi.

Related Articles

Back to top button