Nkhani

Woima ndi pulezidenti azikhala wotani?

Mwezi wa June 2025 onse ofuna kudzapikisana nawo pa chisankho cha Pulezidenti adzakhala akupereka kalata zawo ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) koma asadatero amayenera kusankha munthu wodzaima naye.

Malingana ndi akadaulo pa ndale komanso mbiri, ili ndi gawo lalikulu pa ulendo wopita ku chisankho chifukwa wosankhidwayo amasunga kabali wa chitukuko choncho amayenera kukhala munthu wa masomphenya.

A Chakwera adaleka kutuma wachiwiri wawo a Chilima

Mmbuyomu takhala tikuona kuti akapambana pa chisankho, atsogoleri a dziko lino amaika kumbali amene adaima nawo. Ndipo nthawi zambiri ikafika nthawi ya chisankho chotsatira, iwo amakasankha munthu wina.

Kadaulo pa ndale a Ernest Thindwa ati nthawi zambiri chitukuko sichioneka chifukwa woyimirira pa upulezidenti sayang’ana masomphenya amunthu koma kuthekera kwake kubweretsa mavoti.

Iwo ati izi zili choncho chifukwa dziko la Malawi lidakhazikitsa kale malingaliro ovota potengera mtumdu ndi chigawo chochokera posalabadira ngati munthu yemwe akupatsidwa mpandoyo angaukwanitse.

“Chomwe chimatipweteka n’kusaka mavoti osati nzeru ndi kuthekera kwa munthu. Andale chomwe amaika patsogolo n’kuti kodi munthuyo ali ndi mavoti angati kumsana kwake.

“Mudzaona kuti woimirira pa mpando wa Pulezidenti amakhala ndi funso limodzi loti ndani angandithandize kulowa muofesi osati ndani angadzandithandize kuyendetsa ofesi,” atero a Thindwa.

Kadaulo pa mbiri a Chrispine Mphande a ku sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University ati limeneli ndilo vuto lomwe limabwezera chitukuko mmbuyo chifukwa kulowa m’boma kukatha, ubale wa awiriwo umatembenuka.

“Sikuti ndi themberero kuti Pulezidenti ndi wachiwiri azisemphana ayi koma kuti kagwiridwe kawo ka ntchito n’kosiyana, wina amatha kungokhala ndi gulu kumbuyo kwake koma palibe chomwe amadziwapo,” atero a Mphande.

Iwo ati nthenya imeneyi ikadatha kulumikizika pakadakhala ndondomeko yokhazikika yosankhira woima ndi Pulezidenti kuti nthawi yake isadafike azikhala atasulidwa pa zofuna za ofesi yake.

A Mphande ati pali zitsanzo zambiri zomwe oimirira chipani pa mpando wa Pulezidenti akasankhidwa ku kovenshoni, iwo amakatenga munthu yemwe aliyense samayembekezera n’komwe kuti aime naye.

“Limenelo ndi vuto lalikulu lofunika kukonza. Ngakhale munthuyo atakhala ndi nzeru koma mamembala ena sakhala okonzeka kugwira naye ntchito pomwe patakhala ndondomeko, aliyense akhoza kukhaliratu ndi chiyembekezo n’kudzikonzekeretsa kudzagwira ntchito ndi osankhidwayo,” atero a Mphande.

Mwezi wa August ndi September 2024, zipani zambiri zikhala ndi makovenshoni komwe adindo m’mipando yosiyanasiyana adzasankhidwe koma mpando wokhawo wa wodzaima ndi pulezidenti amasankha ndi wodzaimilira pa upulezidenti basi.

Pachifukwachi, a Mphande ati n’kofunika kuti wosankhayo aziunikiridwa ndi anzake ku chipani chomwe akuimirira komanso akadaulo pa za munthu woyenera yemwe angadzamuthandize kuyendetsa dziko mosavuta.

“Kusaka mavoti kuli apo, nthawi zina kupanga zinthu molondola kumabweretsa mavoti pa kokha koma kungotengera kuti mavoti a lero ndi lero basi n’zija m’mawona kuti nthawi pang’ono anthu ayamba kale kung’ung’udza,” atero a Mphande.

Pomwe a Bakili Muluzi ankasiyira mpando malemu Bingu Wa Mutharika, adawasankhira a Cassim Chilumpha ngati woima nawo ndipo awiriwo sadathe kugwira ntchito limodzi.

Ulendo wotsatira,a Mutharika adasankha mayi Joyce Banda koma ubale wawo udawawasa mkati mwa ndime, nthawi yomwe DPP imabwerera m’boma motsogozedwa ndi a Peter Mutharika, a Mutharikawo adasankha malemu Saulos Chilima ngati woima nawo koma nawonso sadamalize bwino teremu yawo.

Ndipo ulendo wotsatira mu 2019, a Mutharika adadzidzimutsa anthu pomwe adasankha a Evertone Chimulirenji ngati woima nawo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button