Womuganizira kugula mwana wa chialubino afera m’chitokosi

Mmodzi mwa anthu omwe akuzengedwa mlandu wozembetsa mwana wa chialubino wa zaka 14 m’boma la Dedza adamwalira Lachinayi ali m’manja mwa apolisi mzinda wa Lilongwe.

Imfa ya Buleya  Luke idadza pomwe Amalawi ambiri adali ndi chiyembekezo kuti iyeyu ndi yemwe angaulule komwe kuli msika wa ziwalo za anthu achialubino chifukwa mlanduwu umamukhudza kuti ndi amene adagula Goodson Makanjira wa zaka 14 wa m’mudzi mwa Mphanyama kwa Chilikumwendo m’boma la Dedza kuchokera kwa bamboo ake omupeza ndi mnzawo wina.

Koma mwatsoka, Luke yemwe adaonekera m’bwalo la milandu laling’ono ku Lilongwe Lachitatu adamwalira ataukana mlanduwu.

Ndipo mneneri wa polisi m’dziko muno adatsimikiza za imfa ya bamboyu.

Kufa kwa Luke kwadabwitsa bungwe loyang’anira anthu achialubino m’dziko muno la Association of People with Albinism (Apam) omwe anenetsa kuti imfayi ikufunika kuunikidwa bwino ndi akatswiri pa kafukufuku.

“Izi ndi zobwezeretsa mmbuyo chilungamo. Munthu yemwe akuganniziridwa kutengapo gawo lalikulu pa kusowa kwa achialubino afa bwanji ali m’chitokosi asadaulure komwe adamugulitsa Goodson?”adatero mtsogoleri wa bungwelo Overstone Kondowe.

Iye adati bungwe lake likuganizira kuti pali china chake ndithu chomwe chikuchitika chifukwa zonga izi zidachitikanso pa milandu ina iwiri ya anthu a mtunduwu.

Bwalo la milandu la Lilongwe lidayamba kumva Lachitatu pa February 20 pa milandu yokhudza kusowa kwa Makanjira.

Apatu n’kuti Luke ali wefuwefu n’kumachita zodabwitsa m’bwalolo monga kugona pansi, kuwauza apolisi kuti akuchita chizungulire komanso kupempha madzi akumwa.

Woweruza Viva Nyimba adayamba kumva kuchoka kwa Kumbilani Patson wa m’mudzi mwa Chiwala m’boma la Lilongwe yemwe ndi bamboo womupeza wa Makanjira ndi Sainani Kalekeni wa m’mudzi mwa Chimphanga m’boma lomwelo.

Awiriwa adavomera kusowetsa Makanjira ndipo adauza bwalo kuti adatumidwa ndi Luke pa mtengo wa K800 000 yomwe adali asadalandire.

Koma Luke adakana kuti sakudziwa chilichonse pa za kusowa kwa mwanayo ndipo adakanso kuti sakuwadziwa makosana awiriwo.

Ndipo woweruza milandu Nyimba adauza Luke kuti anene chilungamo chokhachokha chifukwa anthu awiri omwe adavomera mlanduwo amaloza iyeyo ndipo adalondolera apolisi ku nyumba yake ku Mitundu.

Mlanduwu waimitsidwa kufikira pa March 22.

Share This Post