Zizindikiro za kufa kwa ziwalo

Dotolo wa pa chipatala cha Gulupu m’boma la Blantyre, Lerato Mambulu, wati kufa kwa ziwalo nthawi zambiri kumachitika mwadzidzidzi.

Pachifukwa ichi, kumakhala kovuta munthu kumva kapena kuonetsa zizindikiro zoti afa ziwalo.

“Munthu amatha kungomva kupweteka mutu ngati amumenya mwina ndi chitsulo ndikugwa pansi basi kufa kwa ziwalo n’kukhala komweko,” iye adatero.

Mambulu adafotokoza kuti izi zimachitika kwa anthu amene misempha yawo ya magazi yaphulika mbali ya thupi yomwe yafayo.

Iye adati misemphayi ikaphulika, magazi sayenda kupita ku ubongo zotsatira zake sipakhala kulumikizana kulikonse pakati pa ubongo ndi mbali yomwe sikukufika magaziko.

Dotoloyu adati zinthu zikafika pamenepa mbaliyo imaleka kugwira ntchito.

“Anthu ena amatha kufa ziwalo kapena kusiya kuyankhula kwa maola ochepa okha ndikuchira. Ichi ndi chizindikiro chachikulu cha matendawa,” iye adatero.

Mambulu adati izi zili chomwechi chifukwa anthu oterewa amakhala pachiopsezo chachikulu choti atha kuzakhala ndi vutoli mokhazikika mtsogolo.

Pachifukwa ichi, dotoloyu adati munthu akaona izi, asazitenge mwa chizolowezi kuti ndi momwe ndimachitira, koma athamangire ku chipatala kukapeza thandizo kuti mtsogolo, lisadzakhale vuto lokhazikiza.

Iye adati ngakhale izi zili chomwechi, ndi anthu ochepa okha omwe amatha kuyamba motere.

“Kwa anthu omwe BP yawo imakhala yokwera ndipo amamva kuwawa kwa mutu kwambiri, nkhope imatha kuonetsa zizindikiro zofooka kusonyeza kuti nthawi ina iliyonse, ziwalo zikhoza kufa,” iye adatero.Tsabata ya mawa tizafotokoza zinthu zomwe zimamuika munthu pa chiopsezo cha matenda a kufa kwa ziwalo. 

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.