Nkhani

Zokhoma pa makuponi

Listen to this article

Ndondomeko ya fetereza wotsika mtengo [wa makuponi] chaka chino m’madera ena monga Dedza, Karonga, Zomba komanso Kasungu yatsimikizika kuti magulupu ndi nyakwawa sakulandira nawo ndipo ndi mafumu oyambira pa Sub T/A kupita m’mwamba omwe akulandira.

Potsatira izi, nyakwawa zati uku n’kulakwa popeza iwo sanalembetse m’kaundula pamodzi ndi anthu awo potsatira lonjezo la Pulezidenti Joyce Banda mwezi wa Sepitembala loti mafumu adzalandira fetereza wawo padera ati pofuna kuthana ndi mchitidwe wakatangale.

Ku madera angapo omwe Tamvani yatsimikizira nkhaniyi, mafumu omwe alandira fetereza ndi ma Sub T/A [matumba awiri] ma T/A [matumba 4], ma Senior Chief [matumba 6] komanso ma Paramount [matumba 8].

Apa katswiri pa zandale, yemwenso adachitapo kafukufuku pa za makuponi, Blessings Chinsinga, waunikira kuti ndondomeko ya makuponi chaka chino ikhoza osalongosoka.

Nyakwawa ndi magulupu ndi amene m’mbuyo monsemu amalandira makuponi ku nthambi ya zaulimi m’dera lawo ndipo amakagawira anthu awo kuti azikagwiritsa ntchito ku malo komwe kwafikira feterezayu. Pamakuponiwo akuti pamakhala awiri omwe amakhala a mfumuyo.

Chinsinga wagwirizana ndi magulupu komanso nyakwawa podabwa kuti pakati pa mafumu akuluakulu ndi mafumu aang’ono, osaukirapo moyenera kulandira feterezayu ndani?

Mneneri wa boma, Moses Kunkuyu wati nkhaniyi ndi yodzidzimutsadi ndipo nayenso sakudziwa kuti zidzikhala bwanji, kotero anati afunse kaye Pulezidenti Banda.

“N’zoonadi [kuti sakulandira]. Koma nane ndifunsefunse kaye,” anatero Kunkuyu.

Nduna ya zaulimi, Professor Peter Mwanza idatsimikizira kuti mafumuwa sakulandira feterezayu koma inakana kuyankha mafunso ena.

Nyakwawa Macheso ya kwa T/A Kapeni m’boma la Blantyre yati kumeneko auzidwa kuti salandira.

Lachiwiri pa 23 Okotobala, T/A Kachindamoto ya ku Dedza inati sikudziwa kuti nyakwawa ndi magulupu ziwathera bwanji kumeneko.

Gulupu wina ku Neno anati izi zikutanthauza kuti mafumu aang’ono akuyenera kugula okha fetereza, zomwe sizapafupi.

“Ife timasunga anthu; ndalama zathu n’zochepa ndipo sitingakwanitse kugula fetereza. Apa tingofera dzina la ufumu. Boma litiganizire,” idatero mfumuyi.

Ku Kasungu kwa Mfumu Yaikulu Kaomba akuti ‘oyenerawo’ alandira kale ndipo magulupu ndi nyakwawa sadalandire.

“Kuno tinalandira apulezidenti atangolankhula muja,” anatero Kaomba.

Ku Karonga kwa T/A Kalonga akutinso analandira kale ndipo magulupu ndi nyakwawa chawo palibe.

Gulupu Chisinkha ya m’boma la Mulanje kwa T/A Mabuka yati nkhawa zili biii!

Chinsinga wati apa boma lalephera kuthana ndi mchitidwe wa ziphuphu. Iye wati mafumu oyenera kulandira feterezayu ndi magulupu komanso nyakwawa chifukwa amalandira ndalama zochepa komanso amenewa ndiwo amagawa makuponi kwa anthu.

“Inetu sindidayembekezere kuti zizikhala choncho. Komanso, n’chifukwa chiyani kugawa matumbawo mosiyana?

“Mafumu akuluakuluwa amalandira ma K50 000 pa mwezi pomwe nyakwawa zikulandira K2 500. Mafumu akuluakulu akhoza kugula fetereza. Apatu kuthana ndi ziphuphu sikungatheke,” adaunikira Chinsinga.

Iye adati mafumu akuluakulu amalandiranso ndalama zapadera akatumidwa ndi boma, zomwe sizikuwayenereza kulandira feterezayu.

Maggie Banda wa m’mudzi mwa Msisya kwa T/A Mbelwa ku Mzuzu wati boma liganizire mafumu ang’onoang’ono chifukwa iwo ndi amene amakhala kalikiliki pa ndondomeko ya makuponi.

“Apa ndibwino mafumu akuluakuluwa apereke feterezayo kwa mafumu ang’onoang’ono. Sizili bwino ndipo boma liganizeponso. Sindikukhulupirira kuti ndondomekoyi iyenda bwino,” adaunikira Banda yemwe ndi mlimi wa chimanga kumeneko.

Francis Chingwalu wa m’mudzi mwa Dzomodya kwa T/A Mlauli m’boma la Neno wati akuganiza kuti ndondomeko yachaka chino ikumana ndi mavuto ambiri.

“Otigawira makuponiwa komanso kulemba maina ndi nyakwawa komanso magulupu; kusawapatsa fetereza n’kulakwa ndipo apa tikukhulupirira kuti katangale apitirira ngati boma siliwaganizira,” adatero mkuluyu, yemwe ndi wa komiti pasukulu ya pulayimale ya Ligowe kumeneko.

Related Articles

Back to top button