Front Page

Akana mlandu wosisita ziwalo za mwana wake

Listen to this article

A polisi m’boma la Mwanza anjata ndi kutengera kubwalo la milandu mkulu wina pomuganizira mlandu woseweretsa maliseche a mwana wake wamkazi wa zaka 12.

Mneneri wa polisi ya Mwanza, Victoria Chirwa, wati mkuluyu—yemwe sitimutchula dzina pofuna kuteteza ufulu wa mwana amene akumuganizira kuti adachitiridwa nkhanzayo—waukana mlanduwu atakaonekera kubwalo la magisitireti m’bomalo.

court“Nkhaniyi ibwereranso m’bwaloli tsiku lililonse chifukwa panopa tikufuna tibweretse mboni,” adatero mneneriyu.

Chirwa adauza Msangulutso Lachinayi kuti bamboyu akumuganizira kuti wakhala akusiya mkazi wake akupha tulo iye n’kukalowa m’khitchini momwe mumagona mwanayo n’kumakamuchita zolaulazo.

Adafotokoza Chirwa: “Mayi ake ndiwo adadzadandaula kupolisi kuti bambowa amamuvula mwanayu n’kuyamba kumugwiragwira kumalo obisika. Iwo adauza apolisi kuti bambowa adayamba izi mu January ndipo mwanayu pokwiya adaululira agogo ake zomwe bambo ake ankachita.”

Akuti gogoyo ndiye adafotokozera mayi a mwanayo zomwe adamva ndipo mayiyo adakamang’ala kupolisi.

Koma ngakhale mkazi wa bamboyu pouza Msangulutso watsutsa za nkhaniyi, Chirwa adati apolisi adakanjata bamboyu pa 9 February atamva madandaulo ake.

“Tidamutsegulira mlandu wochitira wina zonyansa (indecent assault). Zimamveka kuti mwanayu adamugonanso, koma izo n’zabodza chifukwa achipatala atampima mwanayu sadapeze kuti adagonedwa, kotero mlandu wogwiririra palibepo,” adatero Chirwa.

Lachitatu Msangulutso udacheza ndi mayiyu komanso mwana wakeyo ndipo onse adati ndi bodza lamkunkhuniza kuti bambo ake adamuvula ndi kumugwiragwira kumaliseche monga zikumvekeramu.

Koma Chirwa adati ngakhale mayiyo wayamba kunena kuti izi sizidachitike, nkhaniyo ipitirirabe kuzengedwa m’bwalo la milandu.

“Angoona kuti nkhaniyi yafika patali komanso mwina sadayembekezere kuti amuna awo anjatidwa. Koma ngakhale zili choncho, nkhaniyo ipitirira ndipo mbali ya boma ibweretsa mboni kubwaloli,” adatero Chirwa.

Msangulutso itampanikiza mayiyo kuti afotokoze bwinobwino mmene nkhaniyi idafikira kupolisi mpaka mwamuna wake kukagona nayo m’chitokosi, iye adati zidafika poti auvomere mlanduwo kaamba koopsezedwa ndi kukakamizidwa ndi anthu okwiya amene adamugwira pomuganizira kuti adachita zopusa ndi mwana wake.

Adafotokoza motere: “Izi zimachitika ndili kumaliro ndipo nditabwerako ndidauzidwa kuti bambowa amakalowa m’khitchini momwe amagona mwanayu.

“Koma nditafufuza mwana adandiuza kuti n’zoona bambo ake amakalowadi m’khitchinino koma ndi cholinga chokamuphunzitsa za kusukulu ndipo amagwiritsa ntchito foni ngati nyali pomuphunzitsapo.

“Atamaliza, adaiwala foniyo pansi pa mphasa pomwe mwanayu amagona. Ndiye adabwerera kukatenga foniyo. Adamudzutsa kuti ayang’ane pansi pa mphasapo,” adatero mayiyo.

Naye mwanayo adanenetsa kuti tate wake ankayang’ana foni basi. “Adakhudza chofunda changa, kenaka adagwira mphasayo ndi kuchotsa foniyo. Sadandigwire,” adatero iye.

Akuti chifukwa chokwiya kuti bamboyu amakalowa m’khitchini mogona mwana usiku mayiyo adapita kwa ankhoswe kuti akamuthandize maganizo.

“Koma nkhani yomwe idamveka ndi yoti bambowa adagwiririra mwanayu, ena akuti adamugwira kumaliseche. Kenaka kudabwera anthu amene adadzawamanga. Kaamba ka mantha iwo adangovomera kuti adachitadi zimenezo ndipo adawatengera kupolisi,” adatero mayiyo, amene akupempha kuti mwamuna wake atulutsidwe.

Pothirapo ndemanga pa zomwe wauza Msangulutso mayiyo, Chirwa akuganiza kuti mayiyu akungosintha mawanga poti iyi ndi nkhani ya m’banja ndipo mwina pali ena akumuopseza kuti asinthe sitetimenti kuti nkhaniyi ikomere mwamuna wakeyo.

“Koma poti nkhaniyi ili m’khoti zikaoneka komweko,” adatero Chirwa.

Mlandu amutsegulira mkuluyu ndi wosemphana ndi gawo 137 la malamulo ndi zilango zake ndipo ngati bwalo lingamupeze wolakwa, akaseweza kundende kwa zaka 14 uko akugwira ntchito ya kalavula gaga.

 

 

Related Articles

One Comment

  1. Bodza bodza bodza. Yemwe akuti anagwililidwa akunena poyela kuti saizowona kuti atate wake anamugwila katundu. Amayi ake nawo atsutsa kuti nkhaniyi inachitikadi. Ndiye mlanduwo a polisi mboni zawo ndi ziti ? Agogo ake a mwanayo omwe sakhala mnyumba momwe milanduyo inachitikila?

    Ngakhale ine siwamalamulo zikuwonetselatu poyela kuti nkhani iyi ndiyovuta kupeza mutu wake. Anzathu a chingelezi amati (it centres on hearsay with no tangible evidence). Zikatero milandu imayendela zomwe odandaula akunena versus zomwe odandaulilidwa akunena. In this case, onse akuti maliseche sanagwilidwe. Mboni palibe. Mayi wa mwana mukuti amagona kuchipinda kenako anali kumalilro, agogo anali kwawo. Palibe anawona bamboyo akutekesa maliseche a mwana.

    Ine ngati jaji, ndikuchita akwiti bambo wa mwana chifukwa choti mlandu ulibe umboni okwanila. Ndikuwadzudzula a polisi chifukwa chotayitsa nthawi ya khoti pobweletsa mlandu opanda umboni okwanila ndipo ndikuwachenjeza a polisiwo kuti akamadzafuna kubweletsanso mlandu oterewu, adzayesetse kusunga umboni monga DNA ya suspect kumaliseche a munthu ogwililidwa olo mmwado wa wogwilidwa.

    Pomaliza ndikuwagamula a polisi kuti apepese bambo yemwe wachititsidwa manyazi mosayenela ndi mbuzi zitatu; imodzi yake, imodzi yamwana wake imodzi ya mkazi wake. Khoti liyime!!!!!!!!!!!

Back to top button
Translate »