Gulewamkulu, agumula sitolo

Gulewamkulu wina Lachwiri lapitalo akumukayikira kuti adagumula sitolo ina pamsika wa Nkhalambayasamba m’boma la Mchinji ndipo akumukaikira kuti adasakaza katundu wa K3.5 miliyoni. Mneneri wapolisiyo, Kaitano Lubrino, Lachisanu adati apolisi amanga anthu 16 amene akuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyo. “Anthu onsewa tikuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi zophwanya sitoloyo komanso kuba katundu,” adatero Lubrino. Malinga ndi Lubrino,…

Milk wastage to drop

The country will start registering a drop in milk wastage following the opening of K1.5 billion milk collecting centre and cooling plant by Lilongwe Dairy Limited at Goliati in Thyolo. Over the years, milk wastage has been a key issue for bulking groups due to unpredictable power supply and poor maintenance of collecting plants. The…

Mangani womenya wotsatira MCP

Chipani chotsutsa cha MCP chapempha apolisi kuti aponye m’chitokosi Isaac Jomo Osman, kadeti wa DPP amene adasautsa ndi kuvulitsa mnyamata amene adavala malaya a chipani chotsutsacho. Lachiwiri m’sabatayi, Osman, yemwe adakhalapo wapampando wa masapota a Big Bullets, adajambulidwa akulamula mnyamatayo amene adavala malaya a makaka a MCP kuti ‘avule ndipo asadzayerekeze kuvala makakawo.’ Izi zidachitika…

Chilima saima nawo

Uli dere n’kulinga utayenda naye. Amene akufuna kuti wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima adzaimire chipanicho pachisankho cha 2019, ati sakutekeseka ndi ganizo lake lofuna kusamuka m’chipani komanso kukana kukapikisa nawo kumsonkhano waukulu. Lachitatu, Chilima adabwera poyera koyamba chibadwireni mpungwepungwe m’chipani cha DPP kunena kuti iye sakapikisana nawo pa msonkhano waukulu womwe uchitike…

Drug resistant TB patients face expulsions

Our Staff Reporter exposes how a group village head expelled her daughter-in-law, a glimpse of discrimination and exclusion of people with multidrug-resistant tuberculosis (MDR-TB). She wanted a happy marriage, but Esther Loleya’s dream was shattered when her mother-in-law sent her packing. The 33-year-old was forced to separate from her husband of three years after being…

Mswahara wa zifukwa

Munga wadza ndi mafinya omwe. Pamene ena akumwetulira kuti boma lakweza mswahara wa mafumu, mafumu ena ati kukwezaku kuwabweretsera mavuto pa ufumu wawo komanso ku boma. Ndondomeko ya zachuma yomwe nduna ya zachuma yabweretsa, boma lati likweza malipiro a mafumu ndi 100 pelesenti ngati aphungu avomereze bajeti imene nduna ya zachuma Goodall Gondwe idapereka m’Nyumba…

Chande says not going back to Nomads

Be Forward Wanderers striker Jaffalie Chande has said he is not going back to the TNM Super League champions. The wayward striker’s latest upshot comes after Wanderers chairperson Gift Mkandawire said last week the team was in talks with the player on his return. “Me, playing for Wanderers? No! That cannot happen. The problem is…

‘Chilonda chatukusira mu DPP’

Bwerani poyera mulankhule kwa Amalawi. Awa ndi mawu a akadaulo pa ndale pamene alangiza mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndi wachiwiri wake Saulos Chilima kuti alankhulepo pa mpungwepungwe omwe wabadwa m’chipanicho. Akadaulowo, Emily Kamanga ndi Henry Chingaipe alangiza izi kutsatira kusamvana pa yemwe atengere chipanicho kuchisankho cha 2019. M’sabatayi, anthu akhala akubwera poyera ndi…

Moto buuu! 2019 yafukiza zipani

Fumbi lachita kobooo! m’zipani pamene kwangotsala chaka chimodzi kuti chisankho cha patatu chichitike m’dziko muno. Chisankho cha patatu chidzakhalako pa 21 May 2019. Izi zili choncho, zikuoneka kuti m’zipani mwabuka moto pomwe nkhondo yolimbirana wodzaimira zipanizo yakula. Pamene ena m’chipani cha DPP akhala akunena kuti Peter Mutharika apereke mpata kwa wachiwiri wake Saulos Chilima kuti…

Akufuna boma likweze malipiro

Bungwe loona za ufulu wa anthu ogwira ntchito la Malawi Congress of Trade Union (MCTU) lapempha boma kuti likweze mlingo wa ndalama zotsikitsitsa zomwe munthu angalandire, komanso kuti anthu amene amalandira ndalama zochepera K50 000 pamwezi asamakhome  msonkho. Polankhula pamwambo wokumbukira tsiku la ogwira ntchito Lolemba ku Lilongwe, mkulu wa bungwelo Luther Mambala adapempha boma…

Amalawi alankhula: Masiku 30, boma liyankhe—Gift Trapence

Malawi adayaka moto dzulo m’zigawo zonse pamene anthu adayenda pokhumudwa ndi ntchito za boma la DPP. Mfundo yamangidwa ndiyoti boma liyankhe m’masiku 30 apo ayi Amalawi abwereranso kumsewu. Mmodzi mwa amene adakonza zionetserozo, Gift Trapence wa bungwe la Centre for the Development of People (Cedep), adati ayembekezera kuti boma liwayankhepasanathe masiku 30. “Pali nkhani zambiri…

‘Mundibwezere voti yanga’, amalawi athafulira APM pazionetsero

Amalawi athera Chichewa mtsogoleri wa dziko lino komanso nduna zake pa zionetsero zomwe zidachitika Lachisau. Zionetserozo zidatsogoleredwa ndi amipingo, amabungwe komanso azipani amene amakakamiza boma kuti liyankhepo pa mavuto amene dziko lino likudutsamo. Mwa zina ndi kuuza mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti athothe nduna ya zachuma Goodall Gondwe komanso ya maboma ang’ono Kondwani…

Madzi achita thope ku DPP

    Madzi sakudikha kuchipani cha DPP pamene mpungwepungwe wolimbirana amene adzatsogolere chipanichi ku chisankho cha 2019 wafika pa kamuthemuthe. Atsogoleri ena a chipanichi anenetsa kuti kaya wina afune kaya asafune, amene atsogolere chipanichi ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika basi, osati wachiwiri wake Saulos Chilima monga ena akufunira. Ofuna Chilima akuti Mutharika, yemwe…

Zipani za moyo zioneke—CMD

  Kodi zipani zinazi zili moyo? Nthawi yofukula yakwana m’zipani pamene bungwe loona mgwirizano wa zipani zosiyanasiyana la Centre for Multiparty Democracy (CMD) lalengeza zokumana ndi akuluakulu a zipani. Bungweli laitana zipani 41 zomwe zidalembetsedwa koma zilibe aphungu m’Nyumba ya Malamulo. CMD ikuchita izi kutsatira kudutsa kwa bilo yokamba za kayendetsedwe ka zipani imene mwa…

Samalani ndi sikelo za chinyengo—MBS

Nthawi yokolola yakwana, pomwe alimi amataya zokolola zawo kwa mavenda akuba amene amamanga sikelo pofuna kuliza alimi. Koma bungwe loona zoyezayeza za malonda la Malawi Bureau of Standards (MBS) lati a malonda akuyenera aonetsetse kuti sikelo zawo zayezedwa ndipo zili pamlingo wabwino. Wachiwiri kwa mkulu wa bungweli Willy Muyila wati bungwe lake ndi lokhalo lomwe…

Akupopa zimbudzi pochepetsa matenda

Ena zimbudzi zawo zikadzadza amagwetsa ndi kukumba china. Uku ndi kutha malo. Lero zinasintha chifukwa khonsolo ya Blantyre mogwirizana ndi Waste Advisers agwirizana zopopa zimbudzi zomwe zadzadza. Iyitu ndi njira yomwe mbalizi zamvana pofuna kulimbikitsa ukhondo mumzinda wa Blantyre pamene matenda a kolera akugwetsa anthu moti kufika lero anthu 26 amwalira. Kupatula izi, khonsoloyi ikuyenda…

Kuli ziii! Pa za mthandizi

Kwangoti zii! Nkhawa yagunda ngati ntchito za mthandizi zomwe anthu amalandira kangachepe akalima msewu ichitike popeza nthawi yake yadutsa osamvapo kanthu. Iyi ndi ndondomeko yomwe anthu amalima misewu ndi kulandira ndalama yomwe imathandiza nthawi ya njala. Chaka chilichonse ntchitoyi imachitika mu January ndi February. Koma pano miyezi itatu yatha mwachinunu, osamva kanthu kuchokera kuboma. Izi…

Chilengedwe chikubwerera ku Mangochi

  Sungapirire mfuu wa mbalame—wopokerezedwa bwino ngati nyimbo m’mitengo yachilengedwe m’boma la Mangochi. Nkhalango yachilengedwe ya m’mudzi mwa Chembe m’boma la Mangochi lero ndi yankho, kutsatira ntchito za Malawi Lake Basin Programme (MLBP) yomwe yamanga chisa kumeneko. Mahekitala atatu amene akhala mbulanda kwa zaka, lero avala pamene alimi alima mpunga wa kilombero komanso kusamala mitengo…

Milandu yachepa ku Blantyre

  Milandu yosiyanasiyana mu mzindawa Blantyre yatsika kuchoka pa 328 mu February chaka chatha kufika pa 204 mwezi omwewo chaka chino, atero apolisi. Wachiwiri kwa mneneri wa polisi mu mzindawo, Dorrah Chathyoka adati iyi ndi nkhani yosangalatsa. “Kutanthauza kuti milandu yomwe anthu amapalamula yatsika ndi 37.8 pa 100 iliyonse. Iyi ndi nkhani yabwino kutsimikizira ntchito…