Nkhani

Ululu podula cha unzika

Listen to this article

Walira mvula waliranso matope. Anthu amene amalakalaka atapeza chiphaso cha unzika mwayi wawagwera koma ayenera akhetse thukuta kuti izi zitheke.

Izi zikudza pamene nthambi ya boma yoona za kalembera osiyanasiyana ya National Registration Bureau (NRB) yayamba kuyenda m’zigawo komwe akuthandiza anthu amene akufuna zitupa za unzika.

Anthu ofuna kukhometsa zitupa za unzika

Kalemberayu akuchitika kuti amene akwanitsa zaka 16 apeze zitupa za unzika komanso kupereka mwayi kwa amene adataya zitupa mwina kuonongeka kuti apeze zatsopano, komanso kulembetsa amene adatisiya.

Nthenda yakula ndi kutalika kwa malo okadulitsira chiphaso zomwe anthu ambiri ati sakwanitsa kutha ndalama kuti akapeze chitupa.

Ndondomekoyi , yomwe yayamba m’maboma a kummwera m’boma la Mzimba, Ntchisi, Ntcheu, Phalombe ndi Nsanje pa 13 January ikuyembekezeka kutha lero pa 27 January.

Ku Ntcheu ndi Nsanje anthu ati akuyenda mtunda woposa makilomita 50 kuti akapeze malo amene akudulitsira chiphaso.

Anthu amene acheza ndi Tamvani m’boma la Nsanje ati mtima wofuna kukhala ndi chiphaso koma thupi likukana kutero chifukwa cha kutalika kwa malo odulitsira zitupa.

Mmodzi mwa anthuwo, a Davis Moses Mnthyola omwe amakhala ku Misamvu m’dera la T/A Tengani m’bomalo ati anthu ambiri alibe mwayi wopeza chitupa cha unzika chifukwa m’dera lawo mulibe malo wolembetserako ziphatsozi. Kuti akalembetse, akuyenda mtunda wautali.

Iwo adati: “Kuno ngakhalenso ku Misamvu, Miliyoni, Kawa, Kamanga, Bwangu, Nandilimbe tikuyenera kupita ku Bangula kapena ku Magoti kwa Sorgin komwe ndi makilomita a pakati pa 37 ndi 42 kuti tikapeze chiphatso cha nzika.

“Ulendowu timalipira K10 000 kupita kokha. Ambiri tapanga chiganizo chosapitako chifukwa ndife anthu ovutika, sitingapeze ndalama imeneyo,” adatero.

A Mnthyola ati atadandaula, adauzidwa kuti kwawoko kulibe magetsi pomwe nthawi ya kalembera wa mavoti pafupifupi dera lililonse kumakhala malo wolembetsera.

“Ndife wokhumudwa. Siife tokha, anzathu a kwa Nthondo akuyenda makilomitala oposa 30 kupita ku Mpatsa pomwe ena ngati aku Nyamigeti akutsetsereka kupita ku Mthawira zomwe zapangitsa ambiri kuti asakhale ndi chidwi ndi ntchitoyi,” adatero a Mnthyola.

A Paul Malora wochokera m’dera la T/A Mlolo ku Nsanje komweko adati n’zokhumudwitsa kuti Mlolo yense bungwelo laika malo atatu okha olembetsera omwe ndi Kalulu, M’bwazi ndi Sankhulani zomwe zikupereka chiopsezo kwa anthu ochokera m’madera ngati Thamboni, Ironi, Mchacha 58, Alufazema ndi ku Masenjere kuti sangakwanitse kulembetsa.

A Malora adati akadakonda bungwelo likadabwereka zipangizo za bungwe la za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) zomwe amapita nazo paliponse potengera kufunikira  kwa chiphatso cha unzika.

Kafukufuku wathu akusonyeza kuti anthu omwe amakhalira kumapiri monga Ching’ o m a , Bambala, Kavulamnthenga komanso Chimzeti akuyenda ndi kutsetsereka mapiri ndi kufika pa sukulu ya pulaimale ya Mchere zomwe achikulire sakukwanitsa chifukwa cha kutalika kwa mtunda.

Wapampando wa mabungwe omwe si aboma ku Nsanje a Mike Dansa apempha bungwe la NRB kuti lichite chilichonse chotheka ndi kuwapatsa malo olembetsera ziphatsozi anthuwa.

“Chiphaso cha unzika n’chaulere ndiye palibe chifukwa choti anthu azionongera ndalama zoposa K20 000 pofuna kukapangitsa chiphaso, uku ndi kupherana ufulu. Ife tikufuna boma lipange momwe amachitira nthawi ya kalembera wa mavoti powapatsa mwayi abale athuwa ndi kuwafikira n’cholinga choti alembedwe masiku omwe adaika asanathe.”

Iwo adati chiphasoch n’chofunika ndipo ambiri ziphatso zawo kumeneko zidapita ndi madzi osefukira.

“Chiphaso cha unzika ndi moyo. Popanda chimenechi munthu sungakhale ndi mtendere popeza uzitengedwa ngati ndiwe wobwera. Boma yesetsani kutithandiza paja kuno anthu ambiri anataya ziphaso zawo ndi anamondwe womwe anabwera pakatipa ngati Ana, Gombe ndi Freddy,” anatero a Dansa.

Izi zili apo, madzi afika m’khosi ku Ntcheu komwe phungu wina kumeneko wayamba kutumi z a galimoto kuti ikatenge anthu a m’dera lake lokha kuti akapeze chiphatso ataona kutalika kwa mtunda.

A Dickson Austin okhala ku Gawaza kwa T/A Phambala adati komwe NRB ikudulitsa ziphaso ndi kwa Senzani komwe ndi mtunda woposa makilomita 50 kupita kokha.

“Galimoto sizifika kuno, yankho ndi njinga ya moto basi ndiye kupita kokha ndi K15 000 kuti ukafike kumsewu wa tala komwe ungakapeze busi, ndiye pobwera uyeneranso upeze ndalama. Tizitenga kuti ndi njalayi?” adadabwa a Austin.

A Joyce Magugu a m’mudzi mwa Njonjo T/A Masasa adati kumeneko kuli anthu ambiri ofuna kupeza ziphatso koma vuto ndi mtunda omwe akuyenda.

“Kuka f ika komwe akudulitsako ndi makilomita 15, tikapita ndiye kuti kubwera ndi usiku chifukwa kukumakhalanso mzere waukulu kuti anthu athandizidwe.

“Ndi bwino akadaonjezera masiku chifukwa kunoko vuto lomwe lakulanso ndi netiweki yomwe siyikudalirira,” adatero.

Ndipo polankhula pasukulu ya sekondale ya Mtowe, phungu wa ku Nyumba ya Malamulo wadera la Nsanje Lalanje mayi Gladys Ganda adamema anthu m’bomalo kuti akalembetse ziphatso za unzika.

A Ganda adati kufunikra kwa ziphatsozi n’kwakukulu ponena kuti ziwathandizira nthawi yopeza zipangizo zotsika mtengo, kukhala umboni wokatsegulira mabukhu a kubanki, kupeza mwayi wopangitsa zitupa zoyendera komanso kudzakhala ndi mwayi wolembetsa m’kaundula wa chisankho kuti adzathe kuvota pa 16 September chaka cha mawa.

Komabe phunguyu yemwe adaperekezedwa ndi gavanala wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) kuchigawo cha kummwera a Thomson Kamangila ndipo amayendera malo ngati Sorgin, Bangula, Phokera, Bagala, paboma la Nsanje, Fargo ndi Mtowe anadandaula ndi momwe ntchitoyi ikuyendera ponena kuti wogwira ntchito ndi wochepa ndipo anapempha nthambi ya NRB kuti ionjezere masiku ogwirira ntchitoyi.

Poyankhapo, mlembi wamkulu ku NRB a Mphatso Sambo anati zonse zikuyenda bwino popeza anthu akulembetsa ziphatsozi.

Iwo anati: “Tili m’gawo lachisanu ya ntchitoyi yomwe tikugwira m’maboma a Nsanje, Phalombe, Ntchisi ndi kumpoto kwa boma la Mzimba. Ntchitoyi tidayamba pa 13 January ndipo idzatha pa 27 January 2024. Awa ndi masiku 15 ndipo tikulembera ziphaso za unzika, ziphatso za omwe anamwalira komanso ziphaso zamabanja.”

Iwo adati m’boma momwe tikugwira ntchito tinatengako magawo 25 pa 100 alionse amene ali m’boma ndipo amasankhidwa mogwirizana ndi a khonsolo ndipo pamakhala malo aakulu amodzi.

“Tikuunguza momwe ntchitoyi yayendera ndipo tikaona kuti n’kofunika kuonjezera masiku a kalemberayu tichita motero. Mukudziwa maboma a Phalombe ndi Nsanje zitupa zambiri zidapita ndi madzi nthawi ya namondwe wa Freddy,” adatero iwo.

Ndipo adaonjeza kuti akatseka kalembera alipoyu, anthu akhoza kupita kumaofesi awo pa boma kapena ku post office.

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button