Nkhani

M’nyamata wa kabaza wapsa

Imfa iliyonse ndi yopweteka, koma yopita munthu wosadwala, ululu wake umakhala waukula kwambiri.

A Jefinala Nyambitani womwe akuwaganizira kuti adanyamula zigubu za mafuta wogulitsa pa njinga yawo ya moto, amwalira imfa yomvetsa chisoni.

Umu ndi m’mene zinthu zidaliri ku Lilongwe

Lipoti likuti a Nyambitani ndi m’nzawo amathamangitsana ndi apolisi omwe amafuna kuwakwizinga kaamba koti adanyamula mafuta ogulitsa m’zigubu.

Mwatsoka adachita ngozi pafupi ndi maofesi a Tobacco  Commission ndipo njinga yawo idayaka moto.

Anthu adakwiya mpaka kuyamba kugenda apolisi.

Apolisi adaponya utsi wokhetsa misonzi pofuna kukhazikitsa bata pa malopo.

Mneneri wa polisi a Foster Benjamin adati a Nyambitani adafera pomwepo pamene m’nzawoyo adathamangira naye ku chipatala cha Daeyang komwe adamutumiza ku chipatala chachikulu cha Lilongwe.

“A Nyambitani ananyamula mafuta womwe adabuka moto atachita ngozi,” iwo adatero.

Anthu omwe adaona ngoziyo ikuchitika adati a Nyambitani amathawa apolisi ndipo adakaombana ndi galimito ina mpaka njinga yawo kuyaka.

Dzina la munthu winalo silikudziwika.

A Benjamin achenjeza oyendetsa njinga kuti asamagulitse mafuta kaamba koti ndi mlandu, komanso mchitidwewu umaika miyoyo yawo pa chiopsezo.

M’dziko muno mwagwa vuto la mafuta zomwe zapereka bizinesi kwa mavenda ndi akabaza omwe akugula petulo pa mtengo wa K5 619 ndi dizilo K5 863 pa lita n’kumakawagulitsa K20 000 pa lita.

Sabata yatha, apolisi ndi a khonsolo ya Lilongwe adapanga kampeni yolanda mafuta kuchokera kwa mavenda.

Mkulu wa khonsoloyo a Clement Stambuli adati adachita izi atalandira madandaulo kuchokera kwa anthu a mu mzindawo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button