ChichewaFront PageNkhani

Kuunika za 2026Mother’s Fun Run

Kampani ya Nation Publications Limited (NPL) ndi abwenzi ake anapeza K672 miliyoni pa liwiro la msangulutso (Mother’s Fun Run) lomwe lidachitika m’mzinda wa Mzuzu Loweruka lapitalo. BRIGHT KUMWENDA adacheza ndi mkulu wa NPL komanso wa MFR a Mbumba Banda kuti amve zambiri.

Banda: Tiyeni tigwirane manja

Mother’s Fun Run (MFR) ya chaka chino yapeza K672 miliyoni. Chisangalalo chanu n’chotani?

Chisangalalo changa n’chodzadza tsaya chifukwa timafuna K500 miliyoni, koma tapeza K672 miliyoni yothandizira zipatala za kumpoto kwa boma la Mzimba. Izi zachitika kaamba ka kudzipereka kwa makampani, mabungwe, mabanki ndi anthu akufuna kwabwino omwe tikugwira nawo ntchito kudzera mu MFR.

Kodi zipatalazo zidali ndi mavuto otani?

Mavuto adalipo a nkhaninkhani. Zipangizo zopititsira patsogolo ntchito zauchembere wabwino zidali zochepa m’zipatala zambiri. Zipatala zina zidalibiretu zipangizo zothandizira amayi oyembekezera pochira. Ngakhale anamwino ndi madotolo akhale ndi luso, sangakwanitse kupulumutsa miyoyo ya amayi ndi ana opanda zipangizo zogwirira ntchito.

Magetsi akathima, komanso madzi akasiya, anamwino ndi madotolo amagwira njakata kaamba koti m’zipatala zambiri mulibe ma generator ndi mathanki osungira madzi. Mwachitsanzo, Mzuzu Urban Community Hospital ndi chipatala chachikulu chomwe chimalandira odwala kuchokera m’zipatala zing’onozing’ono, koma chilibe thanki ya madzi.

Zipatala zina zilibe madzi a m’mipope komanso mijigo moti amayi oyembekezera amayenda mitunda italiitali kukatunga madzi m’mijigo ya m’midzi. Zimbudzi ndi mabafa aukhondo ndi vutonso lalikulu.

Kodi mavuto a m’zipatala za kumpoto kwa boma la Mzimba ndi omwewa?

Ayi, ndi ambiri. Ogwira ntchito ndi galimoto zonyamula odwala n’zochepa. Kumpoto kwa boma la Mzimba kuli anthu oposa 652 692 omwe akugwiritsa ntchito zipatala zoposa 22. Poganizira chiwerengerochi, mutha kuona kuti ambulansi ziwiri n’zosakwanira. Ambulansi zina pafupifupi 10 zidafa, koma ndalama zokonzera palibe. Ndalama zomwe ofesi yaikulu ya m’bomalo imalandira kuchokera ku boma n’zosakwanira kukonzera ambulansi zakufa za m’bomalo. Mvula ikagwa, kumakhala matatalazi chifukwa misewu yambiri ndiyoonongeka komanso yapanda phula. Mayendedwe amavuta ngakhale nthawi ya chilimwe.

Nanga MFR yathandiza motani pa mavutowa?

K672 miliyoni yomwe MFR yapeza yapita ku zipangizo zopititsira patsogolo ntchito za uchembere wabwino. MFR ikupitiriza kuunikira ndi kudandaulira abwenzi ake kuti apitirize kuthandiza zipatala za m’bomalo. Ngakhale MFR yathandiza, sizikutanthauza kuti mavuto atha m’bomalo. Choncho ndikupempha mabungwe ndi anthu akufuna kwabwino kuti apitirize kuthandiza zipatalazo.

Mwachidule, MFR idayamba bwanji?

Titaona kuti imfa za amayi ndi makanda n’zochuluka m’dziko muno, NPL idaganiza zochitapo kanthu. Posinkhasinkha, tidaganiza zoyambitsa liwiro la msangulutso ngati njira yopezera ndalama zogulira zipangizo zothandizira amayi oyembekezera kuchira. Liwiro loyamba lidachitika m’chaka cha 2005 pa chipatala cha Gulupu (Queen Elizabeth Central Hospital) mu mzinda wa Blantyre. Kuchokera nthawi imeneyo, NPL ndi abwenzi ake akhala akuchita liwiro la msangulutso chaka chilichonse kupatula 2019. M’chaka chimenechi tidayamba taima chifukwa cha matenda a korona (Covid-19).

Mwachidule, mu 2023, MFR idali m’boma la Nkhata Bay m’chigawo cha ku mpoto; 2024 idapita ku Chikwawa m’chigawo cha kummwera ndipo chaka chathachi idali ku Kasungu m’chigawo chapakati. Chaka chino yabwerera m’chigawo cha kumpoto—tidali ku Mzimba. Apa mutha kuona kuti MFR ikupindulira zigawo zonse za dziko lino. MFR imapita m’chigawo chomwe chili ndi imfa zambiri za amayi ndi ana.

N’kusintha kotani komwe MFR ikudzetsa?

MFR ikapereka zipangizo pa chipatala, kusintha kumaoneka nthawi yomweyo. Chipatala chimayamba kupereka zithandizo zomwe m’mbuyomu padalibe kaamba ka kusowa zipangizo. Izi zimachititsa kuti chiwerengero cha odwala otumizidwa m’zipatala zikuluzikulu kuchokera m’zipatala zing’onozing’ono chitsike. Izi zimachitika kaamba koti zipatala zing’onozing’ono tsopano zayamba kupereka zithandizo zomwe poyamba zimapeza m’zipatala zikuluzikulu zokha.

Tikapereka zipangizo, odwala amalandira chisamaliro chabwino komanso mofulumira ndipo imfa za amayi ndi ana zimachepa. Anamwino ndi madotolo athu ali ndi luso, koma amasowa zipangizo zopulumutsira miyoyo ya amayi ndi ana. Changu n’chofunika kwambiri pa ntchito zaumoyo chifukwa tikachedwa kupereka chithandizo, miyoyo imataika. Changu chimadza pakakhala ogwira ntchito ndi zipangizo zoyenera.

M’boma la Chikwawa, MFR yathandizira kuti chiwerengero cha amayi othandizidwa mofulumira akakumana ndi mavuto okhudza uchembere chikwere kuchoka pa 89 peresenti kukafika pa 98 peresenti. Pa chipatala chachikulu cha m’boma la Nkhata Bay, chiwerengero cha amayi omwalira ndi uchembere chatsika kuchoka pa 148 kufika pa 83 pa amayi 100 000 alionse. Pa chipatala chomwecho, chiwerengero cha ana omwalira chatsika kuchoka pa ana 14 kukafika 6 pa 1 000 alionse.

Kodi chaka cha mawa MFR ikupita kuti?

Ikupita ku Balaka kaamba koti mavuto a m’bomalo sakusiyana ndi omwe adali kumpoto kwa boma la Mzimba. Masiku akudzawa, tikhala tikulowera kumeneko kuchitira umboni momwe ntchito za uchembere wabwino zikuyendera m’bomalo.

Nanga tsogolo la MFR mukuliona bwanji?

Tsogolo la MFR ndi lowala kaamba koti makampani, mabungwe ndi mabanki adzionera okha kufunika kothandiza pa ntchito za uchembere wabwino. Akamatipatsa ndalama ndi katundu wa MFR, abwenzi athu amafotokoza kufunika kotukula miyoyo ya anthu pa chitukuko cha makampani komanso dziko la Malawi.

Muli ndi mawu otsiriza?

Ndikufuna kuthokoza onse omwe athandiza m’njira zosiyanasiyana pa liwiro la msangulutso la chaka chino. Ndithokozenso ogwira ku kampani ya NPL chifukwa chosatopa komanso kusabwerera m’mbuyo pa ntchito za MFR. Ndi mtima omwewo, tiyeni tipitirize kugwirana manja pamene tikupita ku Balaka.  

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button