Akusaka wopha malume chifukwa cha mtengo
Apolisi ku Chiradzulu akufunafuna bambo wa zaka 35 a Michael Mkandawire, powaganizira kuti adamenya malume ake a zaka 65, a Rodrick Michael, mpaka kufa pa mkangano wokhudza mtengo wa mango.
Izi zidachitika pa 24 October 2026 m’mudzi wa Nanyanga, m’dera la T/A Likoswe, malinga ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ku Chiradzulu a Andrew Kusimbwa.

A Kusimbwa ati amalumewo adasonyeza zofuna kudula mtengo wa mangowo ngakhale abale awo adawalangiza kuti asatero. Komabe, pambuyo pake adaudula mtengowo n’kupita kumalo omwera mowa.
“M’kupita kwawo, mphwawoyo akuti adawaza mtengowo m’zidutswa n’kukabisa m’nyumba mwake,” adatero a Kusimbwa.
Mkanganowo udasanduka wachiwawa pamene amalumewo adabwerera ku nyumba cha m’ma 5 koloko madzulo n’kupeza zidutswa za mtengowo atazibisa. A Mkandawire adathawa n’kukabisala pamene mkanganowo unkakulirakulira, zomwe zidachititsa achibale kumanga amalumewo ndi zingwe pofuna kuwakhazika mtima pansi.
A Kusimbwa adati a Mkandawire pambuyo pake adatuluka komwe adabisala ndipo akuti adayamba kumenya amalume ake ndi nthabwa pamtengo adamangidwapo.
Anthu omwe adalowererapo adamasula a Michael ndi kumulangiza kuti alowe m’nyumba mwake.
M’mawa wa tsiku lotsatira mnzawo wa Michael adawapeza atagona m’nyumba mwawo atamwalira. Abale adakanena nkhaniyi kwa apolisi.
“Akuluakulu a CID adapita ku maloko ndipo adaona zilonda ndi zipsera pa thupi la womwalirayo. Kuyeza kwa mtembo komwe kudachitidwa ku chipatala cha boma cha Chiradzulu kudasonyeza kuti imfayo idachitika chifukwa cha kutuluka magazi mkati mwa thupi chifukwa chomenyedwa” adatero Kusimbwa.



