Nkhani

A Chakwera alephera kukwaniritsa lamulo lawo lomwe

Listen to this article

Akatswiri pa nkhani za chuma ndi ufulu wa anthu adzudzula mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kaamba kolephera kukwaniritsa lonjezo lawo pa nkhani ya maulendo akunja.

Mu November chaka chatha, mtsogoleri wa dziko linoyu analongosola ndondomeko zochepetsera kuonongeka kwa ndalama malingana ndi kuchepa mphamvu kwa ndalama ya kwacha ndi 44 peresenti.

A Chakwera popita ku DRC

Mwa zina, a Chakwera adalengeza kuti aimitsa maulendo awo akunja mpaka March ngati njira yopulumutsira ndalama.

Koma Lachisanu sabata yatha, iwo anapita ku dziko la Democratic Republic of Congo (DRC) kukakambirana ndi mtsogoleri wa dzikolo nkhani zokhudza chitetezo.

Mkulu wa bungwe la Centre for Social Accountability and Transparency a Willy Kambwandira ati zomwe anachita a Chakwera sizikudabwitsa chifukwa aonetsa kuti alibe chidwi chosamalira chuma cha dziko lino.

“Sitikudabwa kuti ngakhale a Chakwera analonjeza kuti aima kaye maulendo akunja kuti ateteze ndalama, akupitirizabe kuyenda. Izi zachititsa kuti ngakhale mabungwe a boma az ichi tanso chimodzimodzi,” iwo adatero.

A K a m b w a n d i r a adati polephera kutsata malamulo omwe adakonza yekha, mtsogoleri wa dziko linoyu wapereka chitsanzo choipa.

“Ngati mtsogoleri wa dziko akuphwanya malamulo ake omwe, zikusonyeza kuti nkhani yoteteza chuma cha dziko lino inali ya mchezo chabe osati yeniyeni. Chifukwa choti Amalawi sakuchitapo kanthu, a Chakwera akamaononga ndalama, sakuwaopanso,” iwo adatero.

Mtsogoleri wa bungwe la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) a Michael Kaiyatsa anati popita kunja kwa dziko lino, a Chakwera ataitsa anthu chikhulupiriro pa nkhani yochepetsa kuonongeka kwa ndalama.

“Kaya ulendo unali wofunikira kapena ayi, achotsabe chikhulupiriro kwa Amalawi. Chimene a Chakwera adakachita ndi kutumiza nduna m’malo mophwanya lamulo lawo lomwe,” iwo anatero.

Nayenso ka d a u l o pa zachuma ku sukulu yaukachenjede ya Catholic University of Malawi a Glynson Chijinthi anati ulendowo sunakwaniritse cholinga chopulumutsa ndalama zakunja.

“Apapa taononga ndalama zambiri zakunja. Komanso ngati mtsogoleri wa dziko akuyendayenda kunja, akuluakulu m’boma naonso aziti ‘nafenso titsatire zomwe mtsogoleri akuchi ta’ . Zikatere, pamakhala chisokonezo chokhachokha,” iwo anatero.

Mneneri wa boma a Mos e s Kun kuyu a n a p e m p h a k u t i atumiziridwe mafunso koma anali asanayankhe pamene timasindikiza nkhaniyi. Koma m’mbuyomu, a Kunkuyu anauza nyuzipepala ya The Nation kuti ulendowo unali wofunikira kwambiri chifukwa anakakambirana ndi mtsogoleri wa dzikolo a Ferlix Tshisekedi nkhani zokhudza chitetezo.

Related Articles

Back to top button
Translate »