Nkhani

‘Osasekerera aphunzitsi ofuna za dama ndi atsikana’

Bungwe loona za maphunziro la Civil Society Education Coalition (Csec) lapempha boma kuti lisalekere panjira kufufuza nkhani yokhudza aphunzitsi ena a m’sukulu za ukachenjede omwe akuganiziridwa kuti amapempha zisembwere kwa ophunzira aakazi kuti aziwakhozetsa m’kalasi.

M’chikalata chomwe wasaina mkulu wa bungwe la Csec a Benedicto Kondowe komanso wapampando wake a Limbani Nsapato, bungwelo lati zomwe amachita aphunzitsi oganiziridwawo n’kuphwanya ufulu wa ophunzira ndipo mpofunika kufufuza mofatsa.

Nkhaniyo yaphulika zitamveka kuti pali aphunzitsi ena akusuku ya ukachenjede ya Mzuzu University (Mzuni) omwe amakakamiza asungwana kuti azigonana nawo ngati akufuna kuti azikhoza m’kalasi.

“Akuluakulu a sukulu imeneyi, unduna wa za maphunziro ndi ena onse okhudzidwa akuyenera kuunika nkhani imeneyi mwachifatse kuti chilungamo chenicheni chipezeke ndipo zikatero, opezeka olakwa akuyenera alandire chilango chokhwima,” atero kalata ya Csec.

Csec yapemphanso bungwe loona za maufulu ya Malawi Human Rights Commission (MHRC) kuti ikonze bwalo loti anthu adzakambirane nkhani imneyi kuti ngati pali ophunzira ena omwe zotere zidawachitikira koma adalibe mpata woulula adzapezepo danga.

“Izi si nkhani zongosesera kunsi kwa mphasa ayi. N’zofunika zizikambidwa kuti anthu azizidziwa. N’kutheka kuti mchitidwe umenewu ndi waukulu kuposa momwe tikuganizira ndiye mpofunika kupereka mpata woti omwe ali ndi madandaulo adzathe kupereka,” yatero Csec.

Iyo yapitirira kunena kuti mchitidwewu ukuchitika m’sukulu za ukachenjede za boma komanso zomwe si za boma komwe aphunzitsi ena opotoka maganizo amagula chiwerewere kwa ophunzira aakazi posinthanitsa ndi zotsatira za m’kalasi.

Mneneri wa unduna wa za maphunziro a Mphatso Nkuonera ati unduna wa za maphunziro uli mkati mofufuza nkhaniyo kudzera ku utsogoleri wa sukulu ya Mzuni kuti ufufuze zomwe zikumvekazo ngati ndi zoona.

“Pa malamulo a unduna wa za maphunziro, umenewu ndi mlandu waukulu kwambiri moti nditsimikizire Amalawi kuti unduna siusiira pomwepa, tifufuza mpaka chilungamo chitaoneka ndipo akapezeka omwe amachita zimenezi alandira chilango,” adatero a Nkuonera.

Koma a Kondowe auza Tamvani kuti sasiira pomwepa nkhaniyo ayitsatira mpaka mapeto ake adzaoneke chifukwa nthawi zambiri nkhani ikalowa kufufuza, zotsatira zake sizioneka mpaka anthu amaiwala.

“Ndikuona kuti ndi udindo wathu nafenso kutsatira momwe kafukufukuyo akuyendera chifukwa kungokhala pansi, mapeto ake nkhani iyiyi ikhoza kuyiwalidwa pomwe ufulu wa asungwana wosalakwa udaphwanyidwa,” adatero a Kondowe.

Womenyera ufulu wa anthu a Michael Kaiyatsa omwe ndi mkulu wa bungwe la Centre for Humn Rights and Rehabilitation (CHRR) ati nkhani iyi siyofunika kufera m’mazira koma kufufuzidwa mpaka pamapeto pake chifukwa ndi yokhudza ufulu wa anthu makamaka asungwana.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button