Nkhani

Amayi ena agundika nkhanza

Listen to this article

Tikamakamba nkhani za nkhanza, nthawi zambiri chala chimaloza abambo. Akati nkhani yogwiririra ndi abambo, kaya ndi yomenya, amene amachita izi ndi abambo.

Komatu amayi enanso si ali olungama pa nkhani za nkhanza. Ndipo ku Zomba, mayi wina ali m’manja mwa apolisi pomuganizira kuti adakoka maliseche a mwamuna wake mpaka kufa chifukwa amamudzudzula pa khalidwe lake la juga.

Ena mwa amayiwo akumangidwa

Palinso nkhani yomwe ili m’khoti ku Mulanje yomwe gogo wina anaotcha manja mdzukulu wake chifukwa chomuganizira kuti anaba ufa wophikira kanyenya.

Lachisanu laliwisiri, apolisi ku Dowa adamanga mayi wa zaka 35, Chimwemwe Kayere pomuganizira kuti adaotcha mwana wake wa zaka 12 chifukwa adaphika mbatata popanda chilolezo.

Malinga ndi mneneri wa apolisi m’bomalo mayi Alice Sitima adati mayiyo ndi amuna ake adapita kumunda ndipo adamusiya mwanayo akugona, ndipo ali uko, mwanayo njala idamupola ndipo adaphika mbatatayo.

Atapeza poto ali pamoto, mayiyo adazaza n’kuotcha mwanayo kenako n’kuthawa.

Ndiye pali nkhani zomwe abambo akusowa mtendere m’mabanja chifukwa chozunzika ndi akazi awo.

Imodzi mwa nkhani zokhumudwitsa kwambiri idatuluka m’nyuzipepala ya The Nation pa 29 September 2022.

Malingana ndi nkhaniyo, bambo wina adadzimangirira chifukwa chozunzika ndi mkazi wake mkaziyo atapeza ntchito. Zinthu zidafika poipa mpaka bambowo adadzimangirira.

Ndiye palinso nkhanza zina zomwe sizikukambidwa kwambiri zomwe amayi ena akumagwiririra ana ang’onoang’ono mopanda manyazi.

Ndiye anthu n’kumafunsa: Amayi oterowa akuchita zimenezi chifukwa chiyani?

Katswiri pa nkhani za jenda a Ngeyi Kanyongolo adavomera kuti amayi amachitanso nkhaza ngakhale kuti zambiri amachita ndi abambo.

“Nkhanza za m’banja sizikukhudza amayi kapena abambo okha chifukwa sizitengera kuti uyu ndi mwamuna kapena mkazi. Aliyense atha kuchita nkhanza,” iwo anatero.

Koma a Kanyongolo anati ngakhale izi zili choncho, kafukufuku akusonyeza kuti abambo ndi omwe amachita nkhanza kwambiri kuposa amayi.

Pa zifukwa zomwe amayi amachitira izi, katswiriyu anati sizikusiyana ndi za amuna monga kukhala ndi mtima woipa, kusakhala ndi luso lothetsera mikangano, mavuto pa moyo wa munthu komanso a ubongo.

“Choncho nkhani iliyonse iyenera kuunikiridwa mwapadera,” iwo anatero.

Nayenso mkulu wa bungwe la Malawi Human Rights Resource Centre yemwenso ndi katswiri pa nkhanizi a Emma Kaliya adati malipoti akusonyeza kuti ngakhale amayi akuchita nkhanza.

“N’chifukwa chake pamene timayamba kampeni imeneyi, tinafunitsitsa kuti abambo azikhalapo chifukwa tinadziwa kuti nawonso akukhudzidwa pa nkhani zochitiridwa nkhanza,” iwo anatero.

A Kaliya anati sakugwirizana ndi maganizo oti umphawi ndi umene umachititsa kuti anthu azichitirana nkhanza.

Iwo anati mabanja ambiri, makamaka m’midzi, ali pa umphawi koma akukhala mwamtendere.

“Pali anthu ena omwe amati munthu akumachita nkhanza chifukwa cha ukali. Koma tiyenera kumafufuza chomwe chimam’pangitsa kuti akhale waukali. Tikatero, ndiye kuti tithana ndi mavutowo.

“Nthawi zambiri chimene chimachititsa ndi mmene munthu anakulira. Ngati makolo samamulangiza, amangochita zinthu zosayenera. Sizitengera kuti ndi mwamuna kapena mkazi koma aliyense,” adatero iwo.

Kadaulo pa kaganizidwe a Ndumanene Silungwe anati nthawi zambiri, amayi omwe amachitira nkhanza amuna kumakhala kubwezera.

“Zimachitika n’zoti mwamuna wakhala akuchita zinthu zosiyanasiyana zosakhala bwino. Mkazi amakhala ngati wabwezera ndipo kumakhala kwakukulu. Nkhanzazi atha kuchitira mwamuna wake kapena ana komanso makolo omwe alibe mphamvu,” iwo anatero.

A Silungwe anati akazi ena sakumachitira chiwembu abale ndi okondedwa awo ndipo m’malo mwake amangozipha.

Iwo adapitiriza kunena kuti nthawi zina amayi amachita nkhanza malingana ndi mmene anakulira. “Palitu anthu ena omwe amakula mwankhanza kapena anali pa chibwenzi chozunza chimene chimachititsa kuti achitire wina nkhanza,” anatero katswiriyu.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button
Translate »