Nkhani

Chepetsani madyo ku maliro

Listen to this article

Zimaoneka ngati nkhambakamwa. Umva adzukulu akana kukumba kumanda chifukwa ndiwo sizinali za nyama. Mbali inayi mafumu kukana kuyendetsa mwambo chifukwa chakudya sichinawafikepo. Nthawi zina a mpingo nawo kuchedwetsa mwambo kaamba ka za ku moto.

Komatu pomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anenetsa kuti dziko lino lili pa mliri wa njala, ndipo kafukufuku wasonyeza kuti anthu 4 miliyoni m’dziko lino ali pachipsinjochi, mafumu ena m’dziko muno agwirizana ndi mfundo yoti anamalira asamakakamizidwe kudyetsa anthu omwe abwera kudzawakuta pa zovuta zomwe zawagwera pozindikira kuti amakhala kale m’mavuto aakulu.

Chaka chino ambiri sakolola kaamba ka ng’amba

Ganizolo lidayamba ndi amfumu a Mwansambo a m’boma la Nkhotakota omwe adaunikira kuti anamfedwa makamaka nyengo ino ya njala akumakhala kakasi akaika maliro chifukwa kangachepe komwe adali nako kapena adapepesedwa nako kamathera kudyetsa anthu.

A Mwansambo adati mosatsukuluza chikhalidwe cha Amalawi, anthu akuyenera kudziguguda pamtima ndikuganizira munthu yemwe wataya mbale wake kenako adyetse nantindi wa anthu odzamukuta.

“Apapa ndi nkhani yongofunika kumvetsetsa kuti mnzathu ali m’mavuto komanso momwe njala yavutiramu, zoona anthu tizilimba mtima n’kusonkhana kuti tidyetsedwe ndi banja limodzi? Chikhalidwe chili apo, tikuyenera kusintha,” adatero a Mwansambo.

Iwo adaunikira kuti pali magulu ena monga alendo operekeza maliro, anamalira amene komanso adukulu a kumanda omwe mpomveka kuwaphikira koma osati munthu aliyense wa pamudzi chifukwa ena akhoza kukadya m’makomo mwawo.

“Apa mpongofunika kuti mafumu amvetsetse ndipo azionetsetsa kuti zovuta zikuikidwa nthawi yabwino osati mpaka tsiku lonse chifukwa kuchedwetsako n’komwe kumachititsa kuti anthu ayambe kuyembekezera chakudya,” adatero a Mwansambo.

Iwo adavomerezanso kuti pali mafumu ena omwe samvera chisoni anamfedwa ndipo mmalo mwake amafuna kuti oferedwawo awasamale kuti awayendetsere bwino mwambo wa maliro koma iwo adati uku n’kulakwa ndipo si mbali imodzi ya chikhalidwe.

A mfumu a Mlolo a m’boma la Nsanje adati mafumu adayamba kalekale kulingalira ndi kumakamba za nkhaniyi koma pamavuta mpofuna kufananitsa pakati pa ufulu wa anamfedwa ndi chikhalidwe pozindikira kuti zonse zimayenera kuyendera limodzi.

“Nkhani imeneyo ndi yofunika kwambiri ndipo takhala tikuikamba kwa nthawi yaitali koma pamavuta mpoti tiilowetsa bwanji mchikhalidwe. Panopa monga momwe mwaneneramo, ndi njala imeneyi n’zosamveka kudalira kuti namalira akudyetseni,” adatero a Mlolo.

Iwo adati kukadakhala bwino kukadakhala kuti mmalo mwa namalira, mudzi ndiwo uzisaka zakudya zapamaliro ngati momwe zinkakhalira mmbuyo kuti namalira akhale ndi nthawi komanso mpata wokwanira wolira mbale wake.

A Mlolo adati mafumu azikhala patsogolo kuongolera anthu awo kuti azimvetsetsa kuwawa kwa zovuta ndi kufunika komugwira mkono namalirayo mmalo moti akatero azipezerapo danga la chakudya.

A mfumu a Kameme a m’boma la Chitipa ati kudera lawo anthu amathandizana wina akagweredwa zovuta koma nawo ati n’zosamveka kuti anamalira azikhala pa chintchito chodyetsa anthu pamaliro.

“Limenelo ndi ganizo lomveka koma ndi longofunika kulikhazikitsa moti anthu asaone ngati mukusintha chikhalidwe chawo. Kale kudali kosavuta chifukwa anthu ankakolola mokwanira kusiyana ndi masiku ano pomwe zinthu zikuvuta,” adatero a Kameme.

Mmodzi mwa akuluakulu wochokera ku nthambi ya za chikhalidwe ku unduna wa maboma ang’onoang’ono, chikhalidwe ndi kuphunzitsa anthu a Humphrey Mpongaminga ati pali zinthu zina zomwe zikhoza kusinthidwa ndi umodzi.

Iwo adati m’Malawi muno chikhalidwe sichisiyana kwambiri pakati pa mitundu kotero kufuna kusintha zinthu ngati kuphika pamaliro n’kofunika mitundu yonse itavomereza chifukwa ngati patakhala kusiyana, ndiye kuti mchitidwewo siungathe.

“Ndi nkhani yongomvana pakati pa mitundu kuti mitundu yonse iziyendera limodzi osati ena ayambitse kenako ena osatsatira ndiye kuti oyambitsa ajanso abwerera mmbuyo,” adatero a Mpondaminga.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button
Translate »