Nkhani

Khonsolo idandaula za mowa wa ‘Ambuye n’tengeni’

Listen to this article

Imodzi mwa nkhani zimene zidayala nthenje sabata yatha ndi ya anthu 8 omwe adamwalira kwa Manase mu mzinda wa Blantyre atamwa mowa wotchedwa Ambuye n’tengeni, khonsolo ya mzinda wa Blantyre yati ikulephera kuthotha ogulitsa mowawu chifukwa alibe ndalama zolipirira apolisi.

Nkhani ndi yoti khonsolo ili ndi udindo woonetsetsa kuti anthu akumwa mowa wovomerezeka ndi cholinga chochepetsa ngozi ngati za mtundu uwu.

Imbibers enjoy their time at a shebeen

Anthu ena akhala akuloza chala khonsolo kuti idalekelera anthu akuononga miyoyo yawo pomwa mowa wosavomerezeka. Malingana ndi malipoti, omwe adaphika mowawo adalibe kalata yowaloleza kuphika kapena kugulitsa mowa mumzinda wa Blantyre.

Koma khonsoloyo yati chala chisamaloze iwo okha chifukwa pali anthu ena omwe ayenera kumatengapo mbali. 

Mkulu wa khonsoloyi a Dennis Chimseu anati akamapita kukayendera ndi kuletsa zinthu monga mowa, amakumana ndi mavuto ambiri monga kuopsezedwa ndi kuvulazidwa.

Iwo anatero: “Tingonena za pompano. Tinapita kwa Manase kuti tikatseke malowo koma anthu anatikonzekera kumeneko. Amafuna kutivulaza ndipo pamene amakolanakolana ndi apolisi, wina anaomberedwa mwendo mwa ngozi.

“Nkhaniyi yapita kukhoti ndipo tilipira ndalama zomwe tidakachitira ntchito zina zotukula khonsolo ino.”

Iwo anadandaula kuti mafumu sakuthandiza kwenikweni chifukwa bwenzi akuwaunikira za kufunika kwa ntchito imeneyo yomwe anati ikuthandiza miyoyo yawo.

Chinthu china chomwe mkuluyu ananena ndi mavuto omwe amakumana nawo akatenga apolisi kuti athandize pa kukwanilitsa malamulo a khonsoloyo.

“Amafuna kulipiridwa choncho ngati tilibe ndalama, timalephera. Sichinthu chapafupi kutenga apolisi chifukwa ndi ndalama zambiri,” iwo anatero ndi kupitilira kunena kuti izi sizikutanthauza kuti asiya kugwira ntchito yawo.

Mphunzitsi pasukulu ya ukachenjede ya Kamuzu University of Health Sciences a Adamson Muula anati vuto lomwe lilipo la mowa wotchipa mtengo ndi loti limapereka chiopsezo pamoyo wa munthu.

“Pali zinthu zina zomwe zimaikidwa m’mowa dala ndi cholinga chokulitsa mphamvu yake. Anthu osauka amakonda zimenezi chifukwa amafuna kuledzera mwachangu.

“N’kofunika kuti anthu azidziwa zomwe zaikidwa. Izi zimakhala bwino kuti azidziwa kuti ndikamwa ichi, zotsatira zake ndi izi,” iwo anatero.

Koma a Muula anadzudzula khalidwe lolephera kukwaniritsa ndondomeko yokhudza mowa ya National Alcohol Policy yomwe boma linakhadzikitsa mchaka cha 2017. Iwo anati ndondomekoyo yakhala ikulandira ndalama zochepa komanso siikuyenda molongosoka.

Nayenso mkulu wa bungwe la Drug Fight Malawi a Nelson Zakeyu anati sikungakhale kovuta kuona mmene mowa umayendera kuchokera kunja ngati ndondomeko ya National Alcohol Policy ingayambe kugwira ntchito yake bwino.

Iwo anati dziko lino lili ndi kuthekera kolimbana ndi mowa, makamaka wotchipa mtengo, ngati ndondomekoyo ingakwanilitsidwe.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button
Translate »