Apulumuka lokumbakumba atadya chiphe kuyesa mpama
Anthu 15 a m’mudzi wa Kalonga mfumu yaikulu Mlolo koma anasamukira kwa Milton TA Mbenje m’boma la Nsanje Lamulungu abwerera lokumbakumba atadwala pambuyo podya ziphe zomwe amaganiza kuti ndi mpama.
A Licius Laelo a zaka 43 anati iwo ndi anzawo a Steven Lodzani a zaka 42 anapita kukakumba mipama ndi kugawana ndi anthu ena potengera kuti kunjaku kuli njala.
Iwo adati: “Anthuwa ataphika kuphatikiza anadya ndipo patapita mphindi 5 anayamba kumva kupotokola m’mimba, kufooka, chizungulire ndipo kenako anayamba kusanza zachikasu. Anthu omwe anayamba kupanga izi analipo 15 kupatula ifeyo ndi mnzanga Lodzani omwenso tinakakumba potengera kuti timadya ku Khonjeni, kwa Kapichi m’boma la Thyolo.”
A Laelo adaonjeza kuti anali ndi mantha kwambiri potengera kuti mudzi wonse umayang’ana iwo ngati omwe tinabweretsa ziphe m’mudzi koma adayamikira a gulupu a Kalonga omwe anawathandiza kwambiri ndi kuwalimbitsa mtima kuti anthuwo akhala bwino.
Mmodzi mwa omwe anadya mpamawo, a Shulva Timoti adati sakufuna kuonanso mpamawu. Iwo adati chifukwa cha njala adatengeka kudya nawo komatu mmene zimatha mphindi 5 amaona dzenje lake lokumbakumba.
A Timoti adayamikiranso a gulupu a Kalonga omwe adamupatsa chithandizo choyamba ndi kumutumiza kuchipatala komanso kumulipilira K7 000 kuchipatala cha a Katchika ku Bangula.
Wina wa amayi omwe anadya nawo mpamawu mayi Joyce Pinifolo a zaka 45 adati zinali zomvetsa chisoni popeza adadya iwowo, ana awiri ndi akazi anzawo.
A Pinifolo anati aphunzira chachikulu kuti kupatula kuti kunjaku kuli njala sakuyenera kudya zinthu zomwe sakuzidziwa potengera kuti nawo abwerera dzenje lokumbakumba.
A gulupu a Kalonga adati ataona izi anasinja makala potengera kuti iwo adaphunzira kuti makala amachepetsa kapena kuthetsa ululu wa ziphe. “Nditasinja makala ndidawapatsa onsewa ufa wa makala kuti abwire. Kenako ndinatenga anyamata a njinga za moto 4 kuwatumiza ku zipatala za Katchika ndi cha boma cha Phokera. Kwa a Katchika ndinalipira K7 000 enawo ndinalipira ndalama K4 000 popita ku Phokera panjinga ya moto iliyonse,” adatero iwo.
A gulupuwo adathokoza phungu waderalo mayi Gladys Ganda kupyolera kwa khansala a Hussein Ngwali popeza anakwanitsa kutitengera anthuwa kubwerera nawo kwawo usiku omwewo. Malingana ndi a Kalonga, njala yafikadi povuta m’deralo ndipo apempha boma, mabungwe ndi akufuna kwabwino kuti awathandize ndi chakudya komanso mbewu popeza nthawi yakwana yoti akabzale kudimba.
Mkulu woona za umoyo m’bomalo Dr. Gilbert Chapweteka anavomereza kuti chipatala chawo cha Phokera chinalandira anthuwa omwe anathandizidwa ndi kubwerera tsiku lomwelo.