Nkhani

Wa zaka 15 amuganizira kupha mchemwali wa 26

Mwana wa zaka 15 ali m’manja mwa apolisi ku Mangochi pomuganizira kuti adazimitsa mchemwali wake wa zaka 26 pa mkangano wa poto woti akazingire chimanga.

Malinga ndi mneneri wa polisi m’bomalo Amina Tepani-Daudi, mwanayo akuti njala itamupola adaganiza zokazinga chimanga kuti mwina angaike kanthu m’mimba.

Kukazinga chimanga siyidali nkhani yolemetsa kwa mchemwali wakeyo koma pamene padakhota ndi poto amene mwanayo amagwiritsira ntchito.

Mwanayo akuti amakazingira chimanga m’poto wa nyuwani amene mchemwaliyo amene lero ndi malemu adagula kumene zomwe zidamuyabwa.

Komabe kwa mwanayo akuti sadaone vuto. Posinthana Chichewa, awiriwo akuti adagwirana m’thupi.

Malinga ndi Daudi, sipadathe nthawi ndipo mwanayo akuti adakatenga mpeni ndi kulasa mchemwaliyo ndipo zidavuta kuti ataketake.

“Apa ndi pamene mwanayo adaganiza zothawa ndipo takhala tikumusaka koma sitimamupeza. Tidafalitsa uthenga kwa anthu athu komanso ofuna kwabwino kuti atithandize kusaka mwanayo,” adatero Daudi.

Iye adati mayi wa anawo adathamanga ndi mtsikanayo kuchipatala kuti akalandire thandizo koma achipatala adasowa pogwira chifukwa n’kuti atamwalira kale.

“Zotsatira za chipatala zidapeza kuti mtsikanayo adatisiya chifukwa adataya magazi ambiri,” adatero Daudi.

Apolisi akhala akusaka woganiziridwayo ndipo amunjata atamupeza m’boma la Balaka komwe ati amabisala pa malo ena ogulitsa mowa. “Tidatsinidwa khutu ndi ofuna kwabwino amene adati mwanayo akuonedwa ku Balaka ndipo tidadziwitsa apolisi ya Balaka amene amunjata. Adamupeza pa malo omwera mowa a Mgawanyemba,” adatero.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button