ChichewaEditors Pick

Asing’anga asowa mtengo wogwira

Listen to this article

 

Chigamulo cha bwalo lalikulu ku Mzuzu kuletsa asing’anga kuti asagwirenso ntchito m’dziko muno zabweretsa mpungwepungwe ndipo asing’anga eniake akuti sakumvetsa chomwe bwaloli likutanthauza.

Lachitatu bwaloli lidapereka chiletso kwa asing’anga kuti asagwirenso ntchito m’dziko muno ponena kuti ndizo zikukolezera kuphedwa kwa maalubino.

Chiletsocho chakhudzanso manyuzipepala ndi nyumba zoulutsa mawu kuti asiye kufalitsa ndi kuulutsa mauthenga a malonda a asing’angawa poti nazonso zikukolezera mchitidwewu.

Loya wa odandaula: Kadzipatike
Loya wa odandaula: Kadzipatike

Chidatsitsa dzaye ndi nkhani yomwe amuna awiri ndi mayi mmodzi a mumzinda wa Mzuzu ataitengera kubwalo lalikululo komwe adakamang’alira asing’anga Masamba Asiyana Mwale ndi Apite Apitana Chiwaya komanso ng’anga zina zogulitsa mankhwala azitsamba ndi kuchita maula kapena zamatsenga ponena kuti anthuwa adawakwangwanula m’njira zosiyanasiyana.

Anthuwa ndi Evans Mponda, Osward Phiri ndi Mary Nyirenda.

Mponda adauza khoti kuti sadachire kumatenda ake atapempha chithandizo cha mankhwala kwa Mwale ngakhale adalipira ndalama zokwana K120 000 atakopedwa ndi zomwe adawerenga munyuzi kuti sing’angayo atha kuthetsa vuto lake.

Naye Phiri adati ali ndi msuwani wake wa zaka 9 ndipo ali ndi nkhawa kuti atha kuphedwa kaamba ka zomwe zakhala zikuwaonekera anthu achialubino   masiku   ano ndi mmbuyomu; pomwe Nyirenda adati Chiwaya adamulonjeza kuti katundu wake amene adabedwa apezeka komanso kuti mwamuna wake amene adamuthawa ukwati abwerera pasanathe sabata, zomwe sizidachitike chonsecho atalipira ndalama zokwana K50 000.

Koma chiletso cha khoti kwa asing’anga onse m’dziko muno sichidakomere mkulu wa bungwe la asing’anga la Traditional Healers, Edward Kayange.

“Ngati pena zalakwika, ndi bwino kukambirana kuti mupeze yankho. Koma zonse zikulankhulidwazi, ife sitikudziwapo kanthu.

“Kodi kuthandiza munthu amene watipeza ndi vuto palakwika? Ndife odabwa ndi chiletsochi,” adatero Kayange, koma sadafotokoze chomwe bungwe lawo lichite.

Woweruza milandu amene adapereka chiletsocho, Dingwiswayo Madise, adati ngati wina ayerekeze kutsutsana ndi chiletso cha bwalolo, ndiye kuti akuyenera kudzayankha mlandu.

Pakalipano, loya wa omwe adakamang’amala kukhoti lalikulu, George Kadzipatike, wati alengeza za chiletsochi m’nyuzi ziwiri zomwe zili ndi awerengi ambiri komanso m’nyumba zoulutsira mawu ziwirinso zomwe anthu amakonda kumvera kuti ng’anga zonse m’dziko muno zidziwitsidwe za chigamulo cha bwalochi.

Dziko lino lataya anthu 17 achialubino kuyambira January chaka chatha ndipo 66 adasowetsedwa kaamba koti anthu ena amaganizo opotoka amakhulupirira kuti mafupa a nthuwa ndi chizimba cha mankhwala olemeretsa.n

Related Articles

Back to top button