Kolera idapha anthu 1 023 pofika lachitatu

Listen to this article

Pomwe nyimbo ya mliri wa kolera ikuimbidwa tsiku ndi tsiku ena n’kumamvera, palinso ena omwe akumanyalanyaza. Pofika Lachitatu lapitali nthendayi idali itapha anthu 1 023 kuyambira pomwe idabuka chaka cha 2022.

 Pofika Lachitatu lomwelo, nthendayo idali idagwira anthu okwana 31 241 ndipo potengera izi, nduna ya zaumoyo yemwenso ndi m’modzi mwa apampando a komiti yoyendetsa za korona komanso kolera a Khumbize Kandodo Chiponda adati n’kofunika kugwirana manja.

 A Chiponda adati akukaikira kuti maikidwe a maliro a anthu omwalira ndi kolera akuonjezera kufala kwa matendawo chifukwa cha kusasamala ndipo adati tsopano azachipatala ndiwo azitsogolera kuika maliro oterowo.

“Ndikuona kuti chifukwa cha kusasamala poika maliro, tizilombo toyambitsa matendawa tikumafala. M’modzi atati watengako kachilombo poika maliro, n’kokwanira kukafalitsa mudzi wonse. Panopa, maliro a kolera akamaikidwa, azitsogolera ndi a zaumoyo,” adatero a Chiponda.

 Kadaulo pa zaumoyo a Maziko Matemba adati n’kofunika kuonjeza magiya pa nkhondo ndi cholinga choti kolera asapitilire.

Iwo ankanena za njira monga kugulitsa ndi kugula zakudya zophikaphika monga nsima, kachewere, mbatata, chimanga ndi mandasi, makamaka pakati pa ana asukulu.

“Apapa mpofunika kuunika bwino chifukwa kungolekelera, kolera ikhoza kumakatengedwa ndi ana n’kumabweretsa m’makomo osazindikira. Tikuyenera kukhala osamala,” adatero a Matemba.

Komiti yoyendetsa korona komanso kolera idapempha makhonsolo kuti atengepo gawo kuonesetsa kuti misika ina yomwe ndiyosalongosoka itsekedwe mpaka patabwera ukhondo okwanira.

M’mbuyomu, unduna wa zamaphunziro udalamula kuti sukulu zonse zisamakhale ndi misika ya zakudya pamalo asukulu ndipo Tamvani adapeza kuti misika yomwe idatsekedwa ndi yapasukulu penipenipo, koma ina yapafupi ndi idakagulitsa malonda a zakudya.

Koma polankhula ndi Tamvani, m’modzi mwa apampando a komitiyo a Wilfred Chalamira Nkhoma adati vuto lina lidapezeka m’malo ogwira ntchito momwe mulibe zimbudzi zaukhondo ndi madzi abwino.

“Izizi takhala tikupempha makampani kuti atengepo mbali chifukwa kolerayu wakhudza aliyense. Ngati antchito angatenge kolera, eni ntchitozo atha kukhudzidwa,” adatero a Nkhoma.

Padakali pano, boma lidalengeza kuti katemera yense wa kolera adatha kotero lidapempha anthu kuti azingodalira ukhondo kuti apewe kuwatenga ndipo lidapemphanso makampani ndi mabungwe kuti athandize ndi zipangizo zopewera kolera.

Related Articles

Back to top button