Kwabwera namondwe wotchedwa Cheneso

Listen to this article

Akadaulo a zanyengo achenjeza kuti zotsatira za mphepo yotchedwa namondwe Cheneso yomwe ikuchokera m’dziko la Madagascar kulowera ku Mozambique zikhoza kukhudza dziko la Malawi.

Akadaulowo, omwe ndi a nthambi yoona zanyengo, ati mphepoyo, yomwe ikuyenda paliwiro la makilomita 15 pa ola, ndiyoopsa ndipo ikhoza kuononga katundu, miyoyo ya anthu ndi ziweto.

Namondwe anagwetsa nyumba zambiri

Nkhaniyi ikubwera pomwe Amalawi akulimbana ndi kusokelera mabala a anamondwe omwe adaononganso zinthu zaka ziwiri zapitazo.

Mu January 2022, mphepo ya namondwe Ana yomwe idachokeraso ku Madagascar komweko kudzera ku Mozambique idaononga katundu wambiri m[‘maboma 20 m’dziko muno.

Chifukwa cha namondweyu, makina opangira magetsi ku Kapichira adaonongeka zomwe zidabutsa vuto la kuthimathima kwa magetsi.

Nkhawayi ili mkati, usiku wa Lachiwiri, mvula ya mphepo yamkuntho idagwa m’madera ena monga ku Lilongwe ndipo mkulu wa nthambi yoona zanyengo a Lucy Mtilatira adati mvulayo ikhoza kukhala namondweyo kapena ziphaliwali.

“Ndamva za mvula ya ku Lilongwe ndipo zikhoza kutheka kuti yabwera kaamba ka namondwe yemwe tikukambayo. Komanso ngakhale nthawi zina ziphaliwali zikanyanya, zimatha kubweretsa mvula ya mphepo,” iwo adatero.

Kalata zomwe nthambi ya zanyengoyo idatulutsa Lolemba komanso Lachiwiri zidachenjeza kuti namondwe Cheneso akhoza kuchititsa kuti mitsinje yambiri isefukire.

Malingana ndi kalatazo, mphepoyo yasakaza kwambiri ku Madagascar ndipo ikulowera ku Mozambique pa liwiro la makilomita 15, koma (liwiroro) likunka likukwera pang’onopang’ono.

“Mayendedwe a mphepoyo akukankha mpweya wachinyontho ndi mphepo zomwe zimabweretsa mvula m’dziko muno. Mwa ichi, tiyembekezere mvula yamphamvu ndi yophatikizana ndi ziphaliwali m’madera ambiri.

“Izi zikutanthauza kuti tiyembekezere kusefukira kwa madzi m’madera ambiri,” zatero kalatazo.

Chiyambireni mvula ya chakra chino, kwaoongeka kale ngozi zochuluka moti anthu 56 adamwalira kale. 30 mwa anthuwo, adamwalira kaamba ka ziphaliwali pomwe 26 adachita kupsinjidwa ndi zipupa zofewa ndi madzi.

Pa 18 January 2023, mkulu wa nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi a Charles Kalemba adati ngozi zamvula ya chaka chino zakhudza kale maanja 16 427 m’maboma 26.

Iwo ati nthambi yawo ili chile kulowera komwe kungagwe ngozi, koma abwereza kupempha anthu kuti azitsatira komwe azanyengo akuunikilira pa momwe nyengo ingakhalire.

Iwo ati anthu akhoza kupewa ngozizo pogwiritsa ntchito zomwe akuunikiridwa komanso zizindikiro zamakolo.

Tikunena pano, zinthu monga misewu, nyumba, sukulu, zipatala ndi zina zaonongeka kale ndipo tili mkati mopereka thandizo komanso kutolera za ngozi zomwe zikugwa.

Related Articles

Back to top button