ChichewaEditors Pick

Mafupa a alubino si chizimba—sing’anga

Listen to this article

Mwadzidzidzi, dziko la Malawi latchuka ndi mbiri yomvetsa chisoni komanso yochititsa manyazi. Iyitu ndi nkhani yozembetsa ndi kupha maalubino ati pokhulupirira kuti mafupa awo ndi chizimba chopezera chuma. Nkhaniyi yautsa mkwiyo waukulu kwa mabungwe, a mipingo, boma, ndi anthu ambiri omwe akuti uku n’kulakwa komanso kuzunza anthu osalakwa. Ambiri amakhulupirira kuti anthu omwe akuchita izi amapita ndi ziwalo za maalubinowa kwa asing’anga kuti akapangire zizimba. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi sing’anga wodziwika bwino mumzinda wa Lilongwe pankhaniyi motere:

Mbewe: Amene akuti mafupa a maalubino  ndi chizimba akunama
Mbewe: Amene akuti mafupa a maalubino
ndi chizimba akunama

Tidziwane wawa…

Ine ndine Dr Mustaf Socrates Mbewe wochokera m’mudzi mwa Sawasawa kwa T/A Chikowi m’boma la Zomba.

Chabwino apa ndakupezani muli jijirijijiri, kodi mukutani?

Pano ndili pantchito yanga. Ine ndine sing’anga ndipo anthu ambiri amandidziwa, monga mukuonera apamu, anthu onsewa akufuna ndiwathandize ndipo si okhawa, ena athandizika ndipo apita kale.

Nkhani yabwino, komatu ine ndili ndi funso. M’dziko muno mwatchuka ndi zopha maalubino ati mafupa awo n’chizimba, n’zoona zimenezi?

Limeneli ndi bodza lamkunkhuniza chifukwa anthu amenewa nchimodzimodzi munthu aliyense kungoti iwo ali ndi khungu loyera. Chimene chija n’chilema chabe koma chilichonse ali ngati mmene munthu adalengedwera.

Nanga mukuona kuti omwe amachita izi amachitiranji?

Anthu amachita izi chifukwa cha zikhulupiriro chabe. Palibe chizimba choti munthu n’kumati akapha alubino ndiye kuti alemera. Zikadatero bwenzi atayamba kulemera makolo kalelo komanso si bwenzi mbadwo uno utapeza alubino ayi chifukwa bwenzi anthu atawamaliza kufuna kulemera.

Nanga poti akuti zizimbazo amapanga ndi asing’anga, inu muti bwa?

Ndanena kale kuti iyi si nkhani yoona, ayi, ndipo ngati alipo asing’anga omwe amachita zoopsa ndi zochititsa manyazizi azindikire kuti kumeneku n’kulakwa chifukwa ngakhale mawu a Mulungu amaletsa kuchotsa moyo ndiye wina aziima pachulu n’kumati ukapha ulubino ulemera? Nzeru zimenezi wazitengera kuti? Ine ndidayamba using’anga kalekale koma sindidalandireko chivumbulutso chimenecho.

Ndiye tiziti omwe amapha maalubinowo amapita nawo kuti?

Choyamba zindikirani kuti anthu ena amangonamizira using’anga asali nkomwe ndiye anthu oterowo ndiwo amanamiza anthu omwe akuwaona kuti azingwitsitsa n’kumawalamula kuti apereke ndalama zankhaninkhani. Ena ndi aja amanamiza ana asukulu kuti ali ndi mankhwala okhozetsa mayeso mapeto ake ana osawerenga kudalira mankhwalawo mapeto n’kudzalakwa mayeso.

Koma mankhwala olemeretsa alipodi?

Chilungamo n’chakuti palibe mankhwala kapena chizimba cholemeretsa koma munthu akalimbikira ntchito n’kulemera apa ndiye mankhwala otetezera chumacho amapezeka. Mundimvetsetse kuti uku kumangokhala kuteteza chuma osati kuonjezera chuma, ayi.

Nanga zikhulupiriro zina monga zija zoti munthu akagone ndi mayi ake kapena mwana wamng’ono kuti alemere n’zoona?

Ayinso, sizitheka. Kungoti asing’angawo amakhala kuti adya ndalama zambiri za munthuyo ndiye amadziwa kuti mayi ake sangalole komanso akagona ndi mwana wamng’ono apalamula mlandu ndipo amangidwa kenako iye aziti munthuyo waphonya chizimba yekha, cholinga ndalamazo asabweze kwa mwiniyo.

Ndidamvako anthu akunena kuti ena adagona ndi amayi awo kuti apeze chuma, mukutanthauza kuti amenewo ankangobwebweta?

Eee, ndipo sadziwaso chomwe akunena kapena kutanthauza. Mudzafufuze monga mwa ntchito yanuyi, mudzaona kuti sing’anga woteroyo akauza munthuyo zokachita ngati zimenezi amamuuzanso kuti azikalimbikira nthito yake kaya ndi ya kumunda kaya ndi bizinesi ndiye chuma chimachokera mukulimbikiramo, osati poti wagona ndi mayi ake.

Pali mawu ena mwina?

Eya, mawu alipo kwa akuluakulu monga aboma ndi achitetezo kuti akhwimitse malamulo otetezera anthuwa chifukwa mapeto ake, zolakwa zopanga anthu ena, lidzaipa ndi dzina la asing’anga.

Mwina awerengi ena akhoza kukhala ndi mafunso angakupezeni bwanji?

Akhoza kundiimbira foni pa 0999 281 903 kapena 0888 890 957 kapenaso 0111 979 290 olo kungofika ku area 22 ku Lilongwe n’kufunsa adzandipeza ndipo ndidzawayankha mafunso awo.

Related Articles

Back to top button