ChichewaEditors Pick

Kusamala nazale ya fodya

Listen to this article

Pamene alimi ali pakalikiliki kusosa, alimi, makamaka a fodya ali m’malingaliro okonza nazale.

STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi mtsogoleri wa alimi a fodya omwe ndi mamembala a bungwe la Tobacco Association of Malawi (Tama) ku Bolero m’boma la Rumphi Isaac Msiska za kusamalira nazale. Adacheza motere:

Tandifotokozerani kuti pokonza nazale ya fodya mlimi amayenera kuyang’ana zinthu ziti?

Choyamba, popanga nazale ya fodya nkupeza malo omwe ali pafupi ndi madzi chifukwa nazale ya fodya imafuna kuthirira kawiri tsiku lililonse osaphonyetsa. Pamafunika kuthirira mmawa kenako madzulo ndiye ngati yatalikirana ndi madzi, pali vuto lalikulu zedi pamenepo.

Alimi amayenera kuyang’anira bwino fodya pa nazale
Alimi amayenera kuyang’anira bwino fodya pa nazale

Malo apezeka, chotsatira nchiyani?

 

Malo akapezeka pamafunika kuonetsetsa kuti mpofewa. Ngati pali polimba, ntchito ya madzi ija imayambira pamenepo kuwazapo kuti pafewe kenako nkugaulapo bwinobwino. Tikatha kugaula, timayikapo zinyalala nkutentha kaamba kuti ngati m’nthaka mumakhala njere za mbewu zina zomwe sizifunika kumerera limodzi ndi fodya zife.

Zonsezi zatheka chimatsatira nchiyani?

Iyi ndinthawi yoyamba kupanga mabedi ndipo popanga mabediwo palinso zina zomwe timayenera kutsatira. Timatenga madzi nkuthiramo mankhwala omwe amathandiza kupha kapena kuthamangitsa

Nyerere zomwe tikazilekerera zimakoka njere tikabzala. Tikawazapo, timapanga mabedi a nazale ya fodya kuyembekezera kuti nthawi ina iliyonse tifesa fodya panazale.

Tsiku lofesa kumakhala zotani?

Tsiku lofesa pamafunika kuti zinthu zonse zofunikira ngati zija ndalongosolazi zikhale pafupi koma china chomwe sindidanenepo ndi udzu waa kansichi otchingira pamwamba pa mbewu zathu. Udzuwu ndi wachilengedwe koma umayenera kukhala pafupi oduladula kale kuti tikangofesa, nthawi yomweyo titchinge pamwamba.

Mumafesa bwanji?

Choyamba kansichi wathu ali apo, timatenga kheni yothiririra nkuyikamo madzi ndi mbewu ya fodya nkumachita ngati tikuthirira ndiye mbewu zimatulukira limodzi ndi madzi aja. Tikatha timatchingira bwinobwino ndi kansichi uja. Tikatero, ntchito yothirira yayambika ndipo timati uku tikuthirira nazale, kwinaku tikukonza kumunda kupangiratu mizere kuti tizichepetsako ntchito ina pang’onopang’ono.

Nazale yabwino imafunika kukhala ndi mabedi angati?

Nazale ikhoza kukhala ndi mabedi angapo koma pamakhala bedi limodzi lomwe limakhala kholo. Zonse timafesa pabedi la kholo lija pofuna kuchepetsa ntchito malinga ndi zomwe ndanena kuti pamakhala kuthirira mwakathithi. Mbande zikakula pang’ono, timazisamutsira pa mabedi ena aja kuti zizipuma bwino koma kuthirira mwakathithi kumapitirirabe.

Nzololedwa kubwereza malo a nazale potengera kuti malo opezeka madzi ndi wovuta?

Nzosaloledwa kubwereza malo a nazale. Mbewu zina zimakhala ndi matenda akeake ndiye mukachotsapo, matenda kapena tizilombo timatsalira pamalopo choncho podzabzala mbewu

Inayo imakumana ndi vutoli ikadali yaing’ono kwambiri nkuvutika kakulidwe.

Pomaliza penipeni, nthawi yabwino kupanga nazale ndi iti?

Nthawi yabwino ndi kumayambiriro kwa mwezi wa September kutchera kuti mvula ikamadzayamba, mbande zidzakhale zitafika pamsinkhu owokera kumunda. Kungotsatira izi bwinobwino, mlimi wapita basi zonse zimuyendera bwinobwno popanda zovuta zambiri. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »