MCP, DPP ilipirira amayi osowa ku bungwe la MEC
Zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi Democratic Progressive Party (DPP) zilipirira amayi omwe achite bwino pa zisankho za chipulula, koma akulephera kupereka ndalama zomwe bungwe la Malawi Electoral Commissionm (MEC) likufuna kuti awalowetse m’kaundula wa anthu odzapikitsana nawo pa zisankho za pa 16 Sepitembala.
Patsikulo anthu adzaponya mavoti osankha mtsogoleri wa dziko lino, aphungu a Nyumba ya Malamulo ndi makhansala.
Pocheza ndi mtolankhani wa wailesi ya kanena ya Times a Brian Banda, mlembi wa MCP a Richarda Chimwendo-Banda adati chipani chawo chilipirira amayi omwe sakwanitsa kudzilipirira kuti alowe m’kaundula ya anthu odzapikitsana nawo ya MEC.

“Tidzalipirira amayi onse omwe sakwanitsa kulipira okha, koma ali ndi kuthekera kodzachita bwino pa zisankho za pa 16 Sepitembala.
“Sitikufuna kuneneratu poyera poopa kupereka mwayi kwa anthu ena omwe ali ndi kuthekera kodzilipira,” anatero Chimwendo-Banda.
Nawo a Mary Navicha, mkulu wa amayi mu Democratic Progressive Party (DPP), akuti chipani chawo chakonza ndondomeko yolipira amayi omwe sakwanitsa kudzilipirira ku MEC.
Aliyense yemwe akudzaima nawo pa zisankho akuyenera kulipira ku MEC kuti alowe m’kaundula wa anthu odzapikitsana nawo pa zisankhozo.
Anthu omwe akudzapikitsana pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino adzalipira K10 miliyoni aliyense pamene abambo omwe akudzapikitsana pa mpando wa aphungu a Nyumba ya Malamulo adzalipira K2.5 miliyoni pamene amayi, achinyamata ndi anthu aulumali adzalipira K1 500 000 lomwe ndi theka la ndalamazo.
Abambo omwe akudzapikitsana pa undindo wa makhansala adzalipira K200 000 pamene amayi adzalipira K100 000.
Mabungwe a Oxfam ndi Women Legal Resource Centre (WOLREC) akhala akukambirana ndi MEC komanso zipani za ndale kuti atsitse ndalama zomwe amayi, achinyamata ndi anthu aulumali omwe akufuna kudzapikitsana nawo pa zisankho adzapereke.
“Tidapempha anzathu a MEC kuti atsitse ndalama zomwe amayi azilipira ndipo adatimvera,“ atero a Lingalireni Mihowa, mkulu wa bungwe la Oxfam.
Zipani zambiri za ndale zidamvera pempholo moti amayi, achinyamata ndi anthu aulumali omwe akupikitsana pa zisankho za chipulula za m’zipani apereka theka la ndalama zomwe abambo akulipira.