Achinyamata sakufooka, sakubwerera mmbuyo
Achinyamata, omwe adzapikitsana nawo pa zisankho za makhansala ndi a phungu a Nyumba ya Malamulo pa 16 Sepitembala, maso awo ali patsogolo, sakufooka, komanso sakubwerera mmbuyo.
A Eliza John, omwe akudzaima pa mpando wa khansala wa dera la Mbonechela m’boma la Machinga, ali pakalikiliki kuchititsa misonkhano n’cholinga choti anthu a m’dera lawo adziwe mfundo zawo za chitukuko.
“Masomphenya anga ndikubweretse zitukuku za madzi aukhondo, maphunziro, ulimi wamakono, komanso kutukula ntchito zaumoyo m’dera lathu,” iwo atero.

A Hastings Mapundi, omwe akudzaima pa udindo wa phungu wa dera la pakati la m’boma la Nsanje, nawo maso awo ali patsogolo.
“Maso anga ali patsogolo. Sindikucheukanso kuopa kuphonyana ndi mpando wa phungu wa Nyumba ya Malamulo,” iwo atero.
A Mapundi akufuna kudzathana ndi umphawi, ulova ndi njala zomwe zamanga mthenje m’deralo.
“Anthu ambiri m’dera lino ndi alimi. Choncho ndikufuna kutukula ulimi wothirira, kupeza misika yodalirika ya mbewu, kutukula bizinesi zing’onozing’ono, kupititsa patsogolo maphunziro a ntchito za manja. Izi zidzathandiza kuthetsa umphawi, ulova ndi njala m’dera lathu,” iwo atero.
Masophenya awo sakusiyana ndi a Benjamin Kachikho Simeon, omwe akudzapikitsana nawo pa mpando wa phungu wa m’dera la Thyolo Thava.
“Ndikufuna kuthana ndi mavuto omwe anthu a m’dera lathu akukumana nawo. Ndikadzatenga mpando ndidzalimbikitsa ntchito za manja, bizinesi zing’onozing’ono, ulimi wothirira, masewero ndi maluso osiyanasiyana pakati pa achinyamata,” iwo atero.
A Aaron Chambo, nawo sakubwerera mmbuyo, akufuna mpando wa phungu wa dera la pakati la boma la Mulanje.
“Ndikatenga mpando ndizapereka mphamvu kwa anthu, kudzetsa chitukuko zosiyanasiyana ndi kuchita zinthu poyera,” iwo atero.
A Chambe akuti achinyamata ambiri “achilandira ndipo ali pambuyo pawo nga nga nga chifukwa masomphenya anga akugwirizana ndi awo”.
Iwo akuti anthu a m’dera lawo akufuna zitukuko za maphunziro, zipatala, madzi aukhondo ndi misewu yabwino.
“Umphawi ndi ulova wakula kwambiri m’dera mwathu ndipo ndakonzeka kuthana nazo,” atero a Chambo.
A Aida Adam Kunje, womwe akudzaima ngati khansala m’dera la Sankhwi ku Machinga, apempha anthu kuti awone zitukuko zomwe achita kale m’deralo.
“Anthu ndi mboni kuti ndayambitsa zitukuko za milatho, mijogo, magetsi ndi zina zambiri,” iwo atero.
Ngakhale izi zili chonchi, achinyamata apempha Oxfam ndi Women Legal Resource Centre (WOLREC) kuti awathandize ndi zipangizo zokopera anthu ovota.
Oxfam ndi WOLREC akulimbikitsa achinyamata, amayi ndi anthu aulumali ambiri kuti apikitsane nawo pa zisankho za pa 16 Sepitembala.
Mkulu wa Oxfam a Lingalireni Mihowa alonjeza kuti adzawapatsa zipangizo zokopera anthu akalembetsa m’kaundulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) wa anthu omwe akufuna kudzapikitsana nawo pa zisankho.
A Mphatso Kapito, omwe akudzaima pa mpando wa phungu wa dera la kummwera chakumvuma kwa boma la Machinga, athokoza Oxfam ndi WOLREC chifukwa cha ntchito yotamandika yomwe akugwira.
“Oxfam ndi WOLREC akugwira ntchito yotamandika chifukwa akutilimbikitsa mtima, komanso kutiphunzitsa mmene tingakopere anthu a m’madera mwathu,” iwo atero.