Nkhani

Adandaula kusowa kwa chipatala

Amayi ochokera m’madera a mafumu aakulu Kaphuka ndi Kamenyagwaza m’boma la Dedza apempha adindo kuti ayesetse kumaliza zipatala zomwe zikumangidwa ponena kuti akukumana ndi mavuto poyenda mtunda wautali komanso kuononga ndalama zambiri pofuna kupeza thandizo loyenera.

Mayi Esme Fedricko ati amayi amakumana ndi mavuto ambiri makamaka kwa Chinkombero chifukwa amayenda mtunda wautali kuti akafike ku chipatala cha Bembeke.

MPIMAChikanda: Timayenda mtunda wa utali

Chipatala cha Chinkombero chidayamba kumangidwa m’chaka cha 2000 ndipo chakhala chisakutsegulidwa mwa zina kaamba kosowa madzi komanso zipinda zochirira amayi oyembekezera.

Fedricko adati: “Ife amayi oyembekezera tikuvutika kwambiri. Timagwiritsa paka pa K20 000 ndi K30 000 kuti tikafike ku chipatala cha Bembeke. Tikadakonda chipatalachi chitamalizidwa tsopano. Padakalipano tili ndi chikhulupiliro kuti zinthu sizintha.”

Mavuto omwe amayi akukumana nawo ku deralo akufanananso ndi omwe amayi a m’dera la Khombe kwa Kaphuka pomwe zaka zonsezi amadzuka m’mawa kwambiri kuyenda kukalandira thandizo ku zipatala zomwe zili kutali.

Mayi Stella Chimkanda kuchokera m’mudzi wa Khombe ati kuchedwa kumaliza chipatala kukupitiliza kuika miyoyo ya amayi ambiri pa chiopsezo.

“Timadzuka cha m’ma 4 koloko kupita ku chipatala chaching’ono cha Kaphuka kapena Kasina. Ndife okondwa kuona kuti boma lamanga chipatala kudera lino koma mpaka pano sichikutsegulidwa. Chidayamba kumangidwa 2022 ndiye tipemphe adindo kuti atsirize zovuta zinazo kuti tiyambe kulandira thandizo pafupi,” atero iwo.

Ndipo Mayi Agnes Anthony adati ali ndi chiyembekezo kuti chipatala cha Khombe chithandizanso anthu kupeza ntchito monga ya chitetezo komanso kusamala chipatalacho.

Poyankhulapo pa nkhaniyi, mmodzi wa akuluakulu owona ntchito zomangamanga ku khonsolo ya boma la Dedza a Godfrey Nkhata ati pali zambiri zomwe zikuyenera kukonzedwa kaye zipatalazi asanazitsegulire. “Tivomereze kuti chipatala ngati cha Chinkombero chachedwa kwambiri. Koma monga momwe mwaonera zinthu zina ngati madzi komanso chipinda chochilira amayi zikhala zikumalizidwa chisanathe chaka chino. Chipatala chimasowekera zinthu zambiri kuti chifike poyamba kugwiritsidwa ntchito ndipo tili ndi chikhulupiliro kuti zonse zitheka miyezi ikudzayi.”

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button