Nkhani

Sinodi ya Livingstonia ayisambira m’manja

Likulu la mpingo wa Church of Central African Presbyterian (CCAP) la General Assembly lati sililowerera pa kusemphana komwe kwabuka mu Sinodi ya Livingstonia ya mpingowo.

Kusemphana zochitako kudaonekera poyera Loweruka lapitalo ku msonkhano wa sinodiyo ku Mzimba pomwe mkulu wa sinodi a Jailos Kamisa adatsukuluza mlembi wamkulu a William Tembo pa gulu.

Koma mlembi wamkulu wa mpingo wa CCAP General Assembly mbusa Mwawi Chilongozi ati akuluakulu a sinodiyo akuyenera kutengerana m’kachipinda komata n’kuthetsa kusemphana kwawo pa okha.

“Zimenezo ndi za m’nyumba mwawo ndipo tikuyembekezera kuti akambirana n’kuthetsa kusemphana kenako ife angotiuza momwe zathera. Akalepherana koti n’kufuna mbali yathu atiuza,” atero a Chilongozi.

Kusemphana kwa m’sinodiyo kukusemphana ndi zomwe a Chilongozi adanena kuti atsogoleri a m’masinodi adagwirizana kuti nkhani zokhudza kusemphana maganizo zizikambidwa m’kachipinda komata.

Achilongozi adanena izi pa msonkhano wa atolankhani wolengeza za chikondwerero choti mpingowo watha zaka 100 ukutumikira m’dziko muno ndipo adati chikondwererocho chidafotsera zonse zoipitsa mpingo.

“Tikudziwa kuti anthu akhala akunena zambiri zokhudza mpingo wa CCAP makamaka pa nkhani ya mikangano koma tsopano zonsenzo ndi mbiri ya kale chifukwa tagwirizana chimodzi chomanga mpingo,” adatero a Chilongozi.

Koma patangotha sabata imodzi chichitikireni chikondwererocho mpomwe atsogoleri a sinodi ya Livingstonia adakadzudzulana pa mbalambanda zomwe sizidakomere akhristu ena.

Ngakhale zili choncho, a Chilongozi ati ndondomeko zotsatira pakakhala kusamvana zilipo koma akuluakulu a m’masinodi satsatira ndipo timadabwa kuti n’chifukwa chiyani.

“Mwachitsanzo, tidagwiritsa ntchito ndondomeko zomwezo kuthana ndi kusemphana kwa sinodi ya Blantyre ndi masinodi ena moti pano sinodiyo idapepesa kwa masinodi enawo nkhani idatha,” atero a Chilongozi.

Ngati kutulo, anthu omwe adali ku msonkhanowo adadzionera a Tembo akukhetsa msozi pomwe a Kamisa amawasambwadza limodzi ndi abusa ena kuti akulowetsa ndale mu mpingo.

“Ndi zoona kuti mpingo umayenera kugwira ntchito yotumikira anthu limodzi ndi boma koma zina zimanyanya. Mwachitsanzo, nthumwi zoposa 50 motsogozedwa ndi mlembi wamkulu zidapita ku nyumba ya boma ku Mzuzu, tamva kuti adachita kuitanidwa ndi boma,” adatero a Kamisa.

Iwo adati chowawa kwambiri n’choti ngakhale nthumwizo zimakaimirira Synod, mlembi wamkulu sadakambirane kalikonse ndi mkulu wa sinodi a Kamisa ndipo izi zidalemba mafunso monga loti kodi adaloleza alendowo ndi ndani?

“Komanso uthenga omwe udakanenedwa ku mkumanowo ngosagwirizana ndi mfundo za Sinodi ya Livingstonia,” adatero a Kamisa.

Iwo adasambwadzanso likulu la sinodi yawo ponena kuti ikulephera ntchito take ndipo adalapa kuti ngakhale dzina lili limodzi, mpingowo ngogawanika.

“Funso n’kumati kodi tikutumikira Chauta yemweyu kapena wina? Ndifedi akazembe a Mulungu? Umodzi wathu udzatha, aliyense akungoganiza zake basi. Izi nzochititsa manyazi, zosaloledwa nzochotsa ulemu,” adatero a Kamisa.

Koma a Tembo adati ngakhale adasambwadzidwa chotero pagulu, sangatule pansi udindo wawo ngati mlembi wamkulu wa Synod ya Livingstonia.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button