Nkhani

Amalawi akulira ndi vuto la magetsi

Amalawi akudandaula usiku ndi usana kaamba ka kuthimathima kwa magetsi komwe akuti kwasokoneza mabizinesi ndi mabajeti m’mabanja chifukwa ena akuopa kuguliratu zinthu zofunika kusunga m’mafiriji.

Tamvani atazungulira m’madera ena mu mzinda wa Lilongwe monga Shire ku Area 49 ndi Nsungwi Lachiwiri adapeza kuti magetsi adali othima ndipo ochita bizinesi zolira magetsi ena adali khale.

A Wilson Chimkombero ali ndi malo omwe amaotchererapo katundu osiyanasiyana ndipo pa tsikulo amangoti zungulizunguli kusowa chochita ndipo adati moyo umenewo umachitika masiku ambiri.

“Kunena zoona, zambiri zasokonekera ngakhale ntchito zayamba kutithawa chifukwa eni ake akabwera kawiri n’kupeza kuti ntchito siyikuoneka, salabadira za magetsi mmalo mwake amangolanda ntchitoyo iwe n’kumaoneka ngati wosatha,” adatero a Chimkombero.

Iwo adaonjeza kuti pa chifukwachi, pena zikumakhala zovuta kulipira antchito okhazikika moti pakali pano adasungako wa ntchito mmodzi pomwe enawo amangogwira nawo mwaganyu ntchitoyo ikapezeka.

“Tikakhala ndi ntchito timachita kulemba aganyu kuti ngati magetsi akuyaka iyende msanga. Pena ntchito yoti mmbuyomo tinkamaliza masiku awiri, pano ikumatha sabata kapena kuposerapo,” iwo adatero.

Nawo a Jane Chimzimu a saluni ku Nsungwi tidawapeza makasitomala ofunika kuumitsa m’mutu atangokhala kudikira magetsi ndipo iwo adati izi zikchepetsa makasitomala awo.

“Nanga kasitomala akumane ndi zimenezi kawiri olo katatu angabwerenso? Pali anzathu amasaluni akuluakulu omwe ali ndi majenereta kapena magetsi a dzuwa komwe makasitomala athu akuthamangira,” adatero a Chimzimu.

Kunena za mabajeti a m’nyumba, mayi Treazer Banda aku Area 25B adati adasiya kuguliratu zinthu ngati ndiwo ndi zina zofunika kusunga m’firiji chifukwa zimawonongeka.

“Tsono enafe tidazolowera kuguliratu zinthu kuti ndalama zikamasowa tisamakhale kakasi, kuti muone m’firiji panopa mupezamo mabotolo a madzi basi chifukwa sadetsa nkhawa,” adatero a Banda.

Koma apulezidenti a Peter Mutharika povomereza kuti kulidi vuto lamagetsi adati Amalawi apilire chifukwa pakutha kwa miyezi 8, vuto la magetsi lidzakhala litatha.

Polankhula ndi anthu ku Nselema Loweruka sabata yatha iwo adati gwero la vutolo ndikukalamba kwa makina opangira magetsi omwe akhalitsa ndiye akulephera kupanga magetsi okwanira.

“Makina ena akhala zaka 60 kapena 70 ndiye sakupanga magetsi okwanira ayi koma tikukambirana ndi mayiko kuti atithandize ndiye poti zimatenga nthawi, mungopilira pakamatha miyezi 8 vutoli lidzakhala litatha,” adatero a Mutharika.

Koma mwezi wa November 2017 muulamuliro wawo woyamba, a Mutharika adalonjezanso kuti pakutha kwa chaka, vuto la magetsi lidzakhala litatha koma mmalo mwake lidankira.

Koma pazakufowoka kwa makina opangira magetsiwo, nduna yazamagetsi a Jean Mathanga adati makinawo adafowoka kaamba koti boma lomwe lapitalo silimawakonza momwe amafunikira.

“Zinthu zambiri ku Escom ndi Egenco ndizakutha kwambiri moti kuthima kwamagetsi sinkhani yokaikitsa koma monga apulezidenti adanenera, tikuyesetsa kuti vutolo lithe,” adatero a Mathanga.

Koma Amalawi ambiri mmasamba amchezo akutsutsa izi ponena kuti muulamuliro womwe wapitawo magetsi samavuta ngati momwe zikukhalira pano ndipo ena ati ndibwino kunena pomwe pali vuto lenileni kusiyana nkuloza zala ena.

“Nthawi zina ndibwino kunena zowona nkupeleka pulani yomwe ilipo kuti vuto lithe, izi zoloza zala maboma ammbuyo sizingabweletse magetsi. Chofunika apapa nkuyika ndalama zokwanira kumphamvu zamagetsiko basi,” atero a Talimba Chisale.

A Macsensio Nkhoma patsamba lomwero ati: “Makina akutha omwe amatipatsa magetsi zaka zisanu zapitawo ndi omwe akubweretsa vuto lero?”

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button